Rute 4:15 - Buku Lopatulika15 Nakhale uyu wakukubwezera moyo, ndi wodyetsa ukalamba wako; pakuti mpongozi wako amene akukonda, amene aposa ana aamuna asanu ndi awiri kukuthandiza, anambala. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201415 Nakhale uyu wakukubwezera moyo, ndi wodyetsa ukalamba wako; pakuti mpongozi wako amene akukonda, amene aposa ana amuna asanu ndi awiri kukuthandiza, anambala. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa15 Mwanayo adzakupatsani moyo watsopano ndipo adzakuchirikizani mu ukalamba wanu. Inde wakubalirani mwana mpongozi wanu amene amakukondani, amene wakuwonetsani kuti akupambana ana aamuna asanu ndi aŵiri.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero15 Mwanayo adzakupatseni moyo watsopano ndi kukuthandizani pa ukalamba wanu. Inde, mpongozi wanu amene amakukondani, amenenso waonetsa kuti ali wopambana kwa inu kuposa ana aamuna asanu ndi awiri, ndiye wakubalirani mwanayu.” Onani mutuwo |