Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Rute 4:14 - Buku Lopatulika

14 Pamenepo akazi anati kwa Naomi, Adalitsike Yehova amene sanalole kuti akusowe woombolera lero; nilimveke dzina lake mu Israele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Pamenepo akazi anati kwa Naomi, Adalitsike Yehova amene sanalole kuti akusowe woombolera lero; nilimveke dzina lake m'Israele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Tsono akazi adauza Naomi kuti, “Ngwodala Chauta amene sadakusiyeni nokha opanda wachibale. Mwanayo dzina lake litchuke mu Israele.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Ndipo amayi osiyanasiyana anati kwa Naomi. “Alemekezeke Yehova, amene lero lino sanakusiyeni nokha wopanda wachibale. Mwanayu dzina lake likhale lotchuka mu Israeli.

Onani mutuwo Koperani




Rute 4:14
13 Mawu Ofanana  

ndipo ndidzakuyesa iwe mtundu waukulu, ndipo ndidzakudalitsa iwe, ndi kubukitsa dzina lako; nukhale iwe mdalitso;


Ndipo anati, Ayamikike Yehova Mulungu wa Ambuyanga Abrahamu amene sanasiye mbuyanga wopanda chifundo chake ndi zoona zake: koma ine Yehova wanditsogolera m'njira ya kunyumba ya abale ake a mbuyanga.


Ndipo anatenganso pakati nabala mwana wamwamuna; nati, Tsopano ndidzamyamikira Yehova; chifukwa chake anamutcha dzina lake Yuda; pamenepo analeka kubala.


Ndipo anansi ake ndi abale ake anamva kuti Ambuye anakulitsa chifundo chake pa iye; nakondwera naye pamodzi.


Kondwani nao iwo akukondwera; lirani nao akulira.


Ndipo chingakhale chiwalo chimodzi chimva chowawa, ziwalo zonse zimva pamodzi; chingakhale chimodzi chilemekezedwa, ziwalo zonse zikondwera nacho pamodzi.


M'zonse yamikani; pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu cha kwa inu, mwa Khristu Yesu.


Tiziyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu, abale, monga kuyenera; pakuti chikhulupiriro chanu chikula chikulire, ndipo chichulukira chikondano cha inu nonse, yense pa mnzake;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa