Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Rute 3:15 - Buku Lopatulika

15 Ndipo anati, Bwera nacho chofunda chako, nuchigwire; nachigwira iye; ndipo anayesa miyeso isanu ndi umodzi ya barele, namsenza; atatero analowa m'mzinda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Ndipo anati, Bwera nacho chofunda chako, nuchigwire; nachigwira iye; ndipo anayesa miyeso isanu ndi umodzi ya barele, namsenza; atatero analowa m'mudzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Tsono Bowazi adauza Rute kuti, “Bwera nacho kuno chofunda wavalacho, uchiyale pansi.” Rute adayala chofundacho, ndipo Bowazi adayesa makilogramu makumi aŵiri a barele, namsenzetsa Rute uja. Tsono Rute adachoka nakaloŵa mu mzinda.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Bowazi anati kwa Rute, “Bwera nacho kuno chofunda wavalacho ndipo uchiyale pansi.” Ndipo atayala, Bowazi anathira makilogalamu makumi awiri a barele ndi kumusenzetsa Rute. Rute anapita nakalowa mu mzinda.

Onani mutuwo Koperani




Rute 3:15
5 Mawu Ofanana  

akalirole, ndi nsalu zabafuta, ndi nduwira, ndi zophimba.


Koma mfulu aganizira zaufulu, nakhazikika m'zaufulu zomwe.


Chifukwa chake, monga tili nayo nyengo, tichitire onse chokoma, koma makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro.


Nagona ku mapazi ake mpaka m'mawa; nalawira asanazindikirane anthu. Pakuti anati, Chisadziwike kuti mkaziyo anadza popunthirapo.


Ndipo pamene anadza kwa mpongozi wake, iye anati, Wapeza bwanji, mwana wanga? Pamenepo anamfotokozera zonse anamchitira munthuyo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa