Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Rute 3:14 - Buku Lopatulika

14 Nagona ku mapazi ake mpaka m'mawa; nalawira asanazindikirane anthu. Pakuti anati, Chisadziwike kuti mkaziyo anadza popunthirapo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Nagona ku mapazi ake mpaka m'mawa; nalawira asanazindikirane anthu. Pakuti anati, Chisadziwike kuti mkaziyo anadza popunthirapo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Choncho Rute adagona ku mapazi a Bowazi mpaka m'maŵa, koma adadzuka kudakali kamdimabe, chifukwa Bowaziyo sankafuna kuti anthu adziŵe kuti mkaziyo adaabwera kopunthira bareleko.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Choncho Rute anagona ku mapazi ake mpaka mmawa, koma anadzuka mmamawa kusanayere chifukwa Bowazi anati, “Aliyense asadziwe kuti kopondera barele kunabwera mkazi.”

Onani mutuwo Koperani




Rute 3:14
8 Mawu Ofanana  

Mbiri yabwino iposa zonunkhira zabwino; ndi tsiku lakumwalira liposa tsiku lakubadwa.


Musabwezere munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa. Ganiziranitu zinthu za ulemu pamaso pa anthu onse.


Chifukwa chake musalole chabwino chanu achisinjirire.


Khalani osakhumudwitsa, kapena Ayuda, kapena Agriki, kapena Mpingo wa Mulungu;


pakuti tikonzeratu zinthu zokoma, si pamaso pa Ambuye pokha, komanso pamaso pa anthu.


Mupewe maonekedwe onse a choipa.


ndipo mayendedwe anu mwa amitundu akhale okoma, kuti, m'mene akamba za inu ngati ochita zoipa, akalemekeze Mulungu pakuona ntchito zanu zabwino, m'tsiku la kuyang'anira.


Ndipo anati, Bwera nacho chofunda chako, nuchigwire; nachigwira iye; ndipo anayesa miyeso isanu ndi umodzi ya barele, namsenza; atatero analowa m'mzinda.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa