Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Rute 3:13 - Buku Lopatulika

13 Gona usiku uno, ndipo kudzali m'mawa, akakuombolera, chabwino, akuombolere; koma ngati safuna kukuombolera, pali Yehova, ndidzakuombolera cholowa ndine; gona mpaka m'mawa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Gona usiku uno, ndipo kudzali m'mawa, akakuombolera, chabwino, akuombolere; koma ngati safuna kukuombolera, pali Yehova, ndidzakuombolera cholowa ndine; gona mpaka m'mawa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Gona konkuno usiku uno mpaka m'maŵa. Ngati iyeyo adzakuloŵe chokolo, chabwino aloŵe. Koma ngati safuna, ndidzakuloŵa ndine, ndikulumbira pamaso pa Chauta wamoyo. Gona mpaka m'maŵa.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Gona konkuno usiku uno mpaka mmawa. Tsono ngati iyeyu adzakulowa chokolo, chabwino alowe. Koma ngati safuna kutero, ine ndikulumbira pamaso pa Yehova Wamoyo kuti ndidzakulowa chokolo. Ugone kuno mpaka mmawa.”

Onani mutuwo Koperani




Rute 3:13
11 Mawu Ofanana  

Ndipo padzakhala kuti, ngati iwo adzaphunzira mwakhama njira za anthu anga, kulumbira ndi dzina langa, Pali Yehova; monga anaphunzitsa anthu anga kulumbira pali Baala; pamenepo ndidzamangitsa mudzi wao pakati pa anthu anga.


Ndipo udzalumbira, Pali Yehova m'zoonadi, m'chiweruziro, ndi m'chilungamo; ndipo mitundu ya anthu idzadzidalitsa mwa Iye, ndipo mwa Iye adzatamandira.


Koma ine ndiitana Mulungu akhale mboni pa moyo wanga, kuti kulekera inu ndinaleka kudza ku Korinto.


Pakuti anthu amalumbira pa wamkulu; ndipo m'chitsutsano chao chilichonse lumbiro litsiriza kutsimikiza.


Ndipo anati, Ndiwo abale anga, ana a mai wanga. Pali Yehova mukadawasunga amoyo, sindikadakuphani.


Nati Naomi kwa mpongozi wake, Yehova amdalitse amene sanaleke kuwachitira zokoma amoyo ndi akufa. Ndipo Naomi ananena naye, Munthuyo ndiye mbale wathu, ndiye mmodzi wa iwo otiombolera cholowa.


Tsopano ndipo, zoonadi, ine ndine wakukuombolera cholowa, koma pali wakukuombolera woposa ine.


Nati Bowazi, Tsiku lomwelo ugula mundawo padzanja la Naomi, uugulanso kwa Rute, Mmowabu, mkazi wa wakufayo, kuukitsira dzina la wakufayo pa cholowa chake.


Ndipo woombolera anati, Sindikhoza kuuombola kwa ine ndekha, ndingaononge cholowa changa; udzitengere wekha mphamvu yanga yakuombola; popeza sinditha kuombola.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa