Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Rute 2:20 - Buku Lopatulika

20 Nati Naomi kwa mpongozi wake, Yehova amdalitse amene sanaleke kuwachitira zokoma amoyo ndi akufa. Ndipo Naomi ananena naye, Munthuyo ndiye mbale wathu, ndiye mmodzi wa iwo otiombolera cholowa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Nati Naomi kwa mpongozi wake, Yehova amdalitse amene sanaleke kuwachitira zokoma amoyo ndi akufa. Ndipo Naomi ananena naye, Munthuyo ndiye mbale wathu, ndiye mmodzi wa iwo otiombolera cholowa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Apo Naomi adauza Rute kuti, “Munthu ameneyo amdalitse Chauta, amene amasunga malonjezo ake kwa anthu amoyo, ngakhalenso kwa anthu akufa.” Ndipo adatinso, “Munthuyo ndi mnansi wathu, mmodzi mwa achibale athu, amene ali ndi udindo wotisamala.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Naomi anati kwa mpongozi wakeyo, “Munthu ameneyu amudalitse Yehova, amene sanasiye kuchitira chifundo anthu amoyo ndi akufa omwe. Anatinso munthu ameneyu ndi mnansi wapaphata. Ndiye ali ndi udindo wotisamalira.”

Onani mutuwo Koperani




Rute 2:20
15 Mawu Ofanana  

Pamenepo Davide anatumiza mithenga kwa anthu a ku Yabesi-Giliyadi, nanena nao, Mudalitsike ndi Yehova inu, popeza munachitira chokoma ichi mbuye wanu Saulo, ndi kumuika.


Ndipo Davide anati, Kodi atsalako wina wa nyumba ya Saulo, kuti ndimchitire chifundo chifukwa cha Yonatani?


Koma ndidziwa kuti Mombolo wanga ali ndi moyo, nadzauka potsiriza pafumbi.


Bwenzi limakonda nthawi zonse; ndipo mbale anabadwira kuti akuthandize pooneka tsoka.


Mbale wako akasaukira chuma, nakagulitsa chakechake, pamenepo mombolo wake, mbale wake weniweni azidza, naombole chimene mbale wake anagulitsacho.


Koma ndinakondwera mwa Ambuye kwakukulu, kuti tsopano munatsitsimukanso kulingirira mtima za kwa ine, kumenekonso munalingirirako, koma munasowa pochitapo.


Ndipo Rute Mmowabu anati, Ananenanso nane ndithu, Uwaumirire anyamata anga, mpaka atatha kucheka zanga zonse za m'minda.


Tsopano ndipo, zoonadi, ine ndine wakukuombolera cholowa, koma pali wakukuombolera woposa ine.


Pamenepo akazi anati kwa Naomi, Adalitsike Yehova amene sanalole kuti akusowe woombolera lero; nilimveke dzina lake mu Israele.


ndipo ndati ndikuululira ichi, ndi kuti, Ugule aka pamaso pa nzika, ndi pamaso pa akulu a anthu a kwathu. Ukafuna kuombola ombola; koma ukapanda kuombola, undiuze, ndidziwe; pakuti palibe woombola koma iwe, ndi ine pambuyo pako. Pamenepo anati, Ndidzaombola.


Ndipo woombolera anati, Sindikhoza kuuombola kwa ine ndekha, ndingaononge cholowa changa; udzitengere wekha mphamvu yanga yakuombola; popeza sinditha kuombola.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa