Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Rute 2:14 - Buku Lopatulika

14 Ndipo pa nthawi ya kudya Bowazi ananena naye, Sendera kuno, nudyeko mkate; nusunse nthongo yako m'vinyo wosasayo. Nakhala iye m'mbali mwa ochekawo; ndipo anamtambasulira dzanja kumninkha tirigu wokazinga, nadya iye, nakhuta, nasiyapo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndipo pa nthawi ya kudya Bowazi ananena naye, Sendera kuno, nudyeko mkate; nusunse nthongo yako m'vinyo wosasayo. Nakhala iye m'mbali mwa ochekawo; ndipo anamtambasulira dzanja kumninkha tirigu wokazinga, nadya iye, nakhuta, nasiyapo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Nthaŵi yakudya Bowazi adauza Rute kuti, “Bwera kuno, udzadyeko buledi ndi kusunsa nthongo yako m'vinyo.” Choncho adakhala pansi pafupi ndi anthu okolola aja, ndipo adampatsa barele wokazinga. Adadya mpaka kukhuta ndipo barele wina adatsalako.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Nthawi ya chakudya cha masana Bowazi anati kwa iye, “Bwera kuno, utenge buledi ndi kusunsa nthongo mu vinyo.” Choncho anakhala pansi pafupi ndi okololawo, ndipo Bowazi anamupatsa chakudya ndi nyama yowotcha. Anadya chilichonse amafuna ndipo chakudya china chinatsalako.

Onani mutuwo Koperani




Rute 2:14
17 Mawu Ofanana  

iwo anabwera nao makama, ndi mbale, ndi zotengera zadothi, ndi tirigu, ndi barele, ndi ufa, ndi tirigu wokazinga, ndi nyemba, ndi mphodza, ndi zokazinga zina,


Mundiyalikira gome pamaso panga m'kuona kwa adani anga; mwandidzoza mutu wanga mafuta; chikho changa chisefuka.


Koma mfulu aganizira zaufulu, nakhazikika m'zaufulu zomwe.


Kodi si ndiko kupatsa chakudya chako kwa anjala, ndi kuti ubwere nao kunyumba kwako aumphawi otayika? Pakuona wamaliseche kuti umveke, ndi kuti usadzibisire wekha a chibale chako?


Ndipo anadya onse, nakhuta; ndipo anatola makombo otsala, nadzala madengu khumi ndi iwiri.


Ndipo ndidzapatsa msipu wa zoweta zanu podyetsa panu; mudzadyanso nimudzakhuta.


Ndipo mudzadya ndi kukhuta, ndi kuyamika Yehova Mulungu wanu chifukwa cha dziko lokomali anakupatsani.


Nati iye, Mundikomere mtima mbuye wanga, popeza mwandisangalatsa, popezanso mwanena chokondweretsa mtima wa mdzakazi wanu, ndingakhale ine sindine ngati mmodzi wa adzakazi anu.


Ndipo ataumirira kukatola khunkha, Bowazi analamulira anyamata ake ndi kuti, Atole khunkha ngakhale pakati pa mitolo, musamchititse manyazi.


nalisenza nalowa kumzinda; ndipo mpongozi wake anaona khunkhalo; Rute natulutsanso nampatsa mkute uja anausiya atakhuta.


Ndipo Yese anati kwa Davide mwana wake, Uwatengere abale ako efa wa tirigu uyu wokazinga, ndi mikate iyi khumi, nuthamangire nazo kuzithando kwa abale ako;


Pomwepo Abigaile anafulumira, natenga mikate mazana awiri, ndi zikopa ziwiri za vinyo, nkhosa zisanu zowotchaotcha, ndi miyeso isanu ya tirigu wokazinga, ndi nchinchi za mphesa zouma zana limodzi, ndi nchinchi za nkhuyu mazana awiri, naziika pa abulu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa