Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Rute 2:11 - Buku Lopatulika

11 Ndipo Bowazi anayankha nanena naye, Anandifotokozera bwino zonse unachitira mpongozi wako atafa mwamuna wako; ndi kuti wasiya atate wako ndi amai ako, ndi dziko lobadwirako iwe, ndi kudza kwa anthu osawadziwa iwe kale.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo Bowazi anayankha nanena naye, Anandifotokozera bwino zonse unachitira mpongozi wako atafa mwamuna wako; ndi kuti wasiya atate wako ndi amai ako, ndi dziko lobadwirako iwe, ndi kudza kwa anthu osawadziwa iwe kale.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Koma Bowazi adayankha kuti, “Zonse zimene wakhala ukuchitira mpongozi wako, kuyambira nthaŵi imene mwamuna wako adamwalira, ndazimva zonsezo. Ndamvanso kuti udasiya bambo wako, mai wako ndi dziko lako, ndipo wabwera kwa anthu amene sudaŵadziŵe ndi kale lonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Bowazi anayankha kuti, “Ine ndawuzidwa zonse zimene wakhala ukuchitira apongozi ako chimwalirire mwamuna wako. Ndamvanso kuti unasiya abambo ndi amayi ako komanso dziko la kwanu ndi kubwera kudzakhala ndi anthu amene sumawadziwa ndi kale lonse.

Onani mutuwo Koperani




Rute 2:11
15 Mawu Ofanana  

Ndipo anauza Davide chimene Rizipa mwana wamkazi wa Aya, mkazi wamng'ono wa Saulo anachita.


Tamvera, mwana wamkaziwe, taona, tatchera khutu lako; uiwalenso mtundu wako ndi nyumba ya atate wako;


Chifukwa chake tsono, yense wa inu amene sakaniza zonse ali nazo, sangathe kukhala wophunzira wanga.


Ndipo m'mene iwo anakocheza ngalawa zao pamtunda, anasiya zonse, namtsata Iye.


Chapafupi nchiti, kunena, Akhululukidwa kwa iwe machimo ako; kapena kunena, Tauka, nuyende?


Nati Naomi, Bwererani, ana anga, mudzatsagana nane bwanji? Ngati ndili nao m'mimba mwanga ana aamuna ena kuti akhale amuna anu?


Potero anagwa nkhope yake pansi, nadziweramira pansi, nanena naye, Mwandikomera mtima chifukwa ninji kuti mundisamalira ine, popeza ndine mlendo?


Yehova akubwezere ntchito yako, nakupatse mphotho yokwanira Yehova, Mulungu wa Israele, amene unadza kuthawira pansi pa mapiko ake.


Nati iye, Yehova akudalitse, mwana wanga. Chokoma chako wachichita potsiriza pano, chiposa chakuyamba chija, popeza sunatsate anyamata, angakhale osauka angakhale achuma.


Nakhale uyu wakukubwezera moyo, ndi wodyetsa ukalamba wako; pakuti mpongozi wako amene akukonda, amene aposa ana aamuna asanu ndi awiri kukuthandiza, anambala.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa