Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Oweruza 9:8 - Buku Lopatulika

8 Kumuka inamuka mitengo kudzidzozera mfumu; niti kwa mtengo wa azitona, Ukhale iwe mfumu yathu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Kumuka inamuka mitengo kudzidzozera mfumu; niti kwa mtengo wa azitona, Ukhale iwe mfumu yathu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Padangotere: mitengo idapita kukalonga mfumu yoti iziilamulira. Ndiye mitengoyo idauza mtengo wa olivi kuti, ‘Iwe ukhale mfumu yathu.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Tsiku lina mitengo inapita kukadzoza mfumu yawo. Tsono mitengoyo inati kwa mtengo wa olivi, ‘Iwe ukhale mfumu yathu.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Oweruza 9:8
8 Mawu Ofanana  

Natumiza Yehowasi mfumu ya Israele kwa Amaziya mfumu ya Yuda, ndi kuti, Mtungwi wa ku Lebanoni unatumiza mau kwa mkungudza wa ku Lebanoni, ndi kuti, Mpatse mwana wanga wamwamuna mwana wako wamkazi akhale mkazi wake; ndipo inapitapo nyama yakuthengo ya ku Lebanoni, nipondereza mtungwiwo.


Ndi Yowasi mfumu ya Israele anatumiza kwa Amaziya mfumu ya Yuda ndi kuti, Mtungwi wa ku Lebanoni unatumiza kwa mkungudza wa ku Lebanoni, ndi kuti, Mpatse mwana wanga wamwamuna mwana wako wamkazi akhale mkazi wake; koma nyama yakuthengo ya ku Lebanoni inapitapo, nipondereza mtungwi.


Ngati phazi likati, Popeza sindili dzanja, sindili wa thupi; kodi silili la thupi chifukwa cha ichi?


Ndipo atamuuza Yotamu, anamuka iye naimirira pamutu paphiri la Gerizimu, nakweza mau ake, nafuula, nanena nao, Mundimvere ine, eni ake a ku Sekemu inu, kuti Mulungu amvere inu.


Koma mtengo wa azitona unati kwa iwo, Ngati ndidzasiya kunona kwanga kumene alemekeza nako Mulungu ndi anthu kukalenga pa mitengo?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa