Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Oweruza 9:2 - Buku Lopatulika

2 Nenanitu m'makutu mwa eni ake onse a ku Sekemu, Chokomera inu nchiti, akulamulireni ana aamuna onse a Yerubaala ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, kapena akulamulireni mwamuna mmodzi? Mukumbukirenso kuti ine ndine wa fuko lanu ndi nyama yanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Nenanitu m'makutu mwa eni ake onse a ku Sekemu, Chokomera inu nchiti, akulamulireni ana amuna onse a Yerubaala ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, kapena akulamulireni mwamuna mmodzi? Mukumbukirenso kuti ine ndine wa fuko lanu ndi nyama yanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 “Funsani nzika zonse za ku Sekemu kuno kuti, ‘Chabwino koposa nchiti kwa inu, kuti ana onse 70 a Yerubaala azikulamulirani, kapena kuti mmodzi yekha azikulamulirani? Muzikumbukiratu kuti paja ine ndine mbale wanu weniweni.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 “Funsani nzika zonse za ku Sekemu kuno, ‘Chabwino ndi chiyani kwa inu kuti ana onse makumi asanu ndi awiri a Yeru-Baala azikulamulirani, kapena kuti azikulamulirani ndi munthu mmodzi basi?’ Kumbukirani kuti ine ndine mʼbale wanu weniweni.”

Onani mutuwo Koperani




Oweruza 9:2
8 Mawu Ofanana  

Ndipo Labani anati kwa iye, Eetu, iwe ndiwe fupa langa ndi thupi langa. Ndipo anakhala naye nthawi ya mwezi umodzi.


Ndipo munene ndi Amasa, Suli fupa langa ndi mnofu wanga kodi? Mulungu andilange naonjezepo ngati sudzakhala chikhalire kazembe wa khamu la ankhondo pamaso panga, m'malo mwa Yowabu.


Pamenepo Aisraele onse anasonkhana kwa Davide ku Hebroni, ndi kuti, Taonani, ife ndife fupa lanu, ndi mnofu wanu.


pakuti tili ziwalo za thupi lake.


Popeza tsono ana ndiwo a mwazi ndi nyama, Iyenso momwemo adalawa nao makhalidwe omwewo kuti mwa imfa akamuononge iye amene anali nayo mphamvu ya imfa, ndiye mdierekezi;


Nakhala nao ana aamuna makumi asanu ndi awiri Gideoni, anawabala ndi iye; popeza anali nao akazi ambiri.


koma mwaukira nyumba ya atate wanga lero lino, ndi kuwapha ana ake, ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, pa thanthwe limodzi; ndipo mwalonga Abimeleki mwana wa mdzakazi wake, akhale mfumu ya pa eni ake a ku Sekemu, chifukwa ali mbale wanu;


Ndipo anamuka kunyumba ya atate wake ku Ofura, nawapha abale ake ana a Yerubaala, ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, pa thanthwe limodzi; koma Yotamu mwana wamng'ono wa Yerubaala anatsalako; pakuti anabisala.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa