Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Oweruza 8:3 - Buku Lopatulika

3 Mulungu anapereka m'dzanja lanu akalonga a Midiyani, Orebu ndi Zeebu, ndipo ndinakhoza kuchitanji monga inu? Pamenepo mkwiyo wao unamlezera, atanena mau awa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Mulungu anapereka m'dzanja lanu akalonga a Midiyani, Orebu ndi Zeebu, ndipo ndinakhoza kuchitanji monga inu? Pamenepo mkwiyo wao unamlezera, atanena mau awa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Mulungu wapereka m'manja mwanu mafumu a Midiyani, Orebu ndi Zebu. Ndachita chiyani kuyerekeza ndi zimene mwachita inu?” Gideoni atanena mau amenewo, anthuwo mitima yao idatsika.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Mulungu wapereka mafumu a Midiyani, Orebu ndi Zeebu mʼmanja mwanu. Ndachita chiyani kuyerekeza ndi zimene mwachita inu?” Atanena izi, anthuwo mitima yawo inatsika.

Onani mutuwo Koperani




Oweruza 8:3
15 Mawu Ofanana  

Kwa ife ai, Yehova, kwa ife ai, koma kwa dzina lanu patsani ulemerero, chifukwa cha chifundo chanu, ndi choonadi chanu.


Pakuti sanalande dziko ndi lupanga lao, ndipo mkono wao sunawapulumutse. Koma dzanja lanu lamanja, ndi mkono wanu, ndi kuunika kwa nkhope yanu. Popeza munakondwera nao,


Mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo; koma mau owawitsa aputa msunamo.


Wosakwiya msanga aposa wamphamvu; wolamulira mtima wake naposa wolanda mzinda.


Mau oyenera a pa nthawi yake akunga zipatso zagolide m'nsengwa zasiliva.


Chipiriro chipembedza mkulu; lilime lofatsa lithyola fupa.


Pakuti m'menemo chonenacho chili choona, Wofesa ndi wina, womweta ndi winanso.


Pakuti ndi chisomo chapatsidwa kwa ine, ndiuza munthu aliyense wa inu, kuti asadziyese koposa kumene ayenera kudziyesa; koma aganize modziletsa yekha, monga Mulungu anagawira kwa munthu aliyense muyeso wa chikhulupiriro.


Ndipo pokhala ife ndi mphatso zosiyana, monga mwa chisomo chipatsidwa kwa ife, kapena mphatso yakunenera, tinenere monga mwa muyeso wa chikhulupiriro;


musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake omposa iye mwini;


Koma ananena nao, Ndachitanji tsopano monga inu? Kodi kukunkha mphesa kwa Efuremu sikuposa kutchera mphesa kwa Abiyezere?


Ndipo Gideoni anafika ku Yordani, naoloka, iye ndi amuna mazana atatu anali naye, ali otopa koma ali chilondolere.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa