Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Oweruza 7:8 - Buku Lopatulika

8 Pamenepo anthu anatenga kamba m'dzanja lao, ndi malipenga ao; ndipo anauza amuna onse a Israele amuke, yense kuhema kwake; koma anaimika amuna mazana atatuwo; ndipo misasa ya Midiyani inali kunsi kwake m'chigwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Pamenepo anthu anatenga kamba m'dzanja lao, ndi malipenga ao; ndipo anauza amuna onse a Israele amuke, yense kuhema kwake; koma anaimika amuna mazana atatuwo; ndipo misasa ya Midiyani inali kunsi kwake m'chigwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Choncho Gideoni adatumiza onse kwao kupatula anthu 300 aja. Tsono osankhidwawo adatenga chakudya ndi malipenga a anthuwo. Zithando zankhondo za Amidiyani zinali chakumunsi m'chigwa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Choncho analola anthu ena onse kuti apite ku nyumba zawo kupatula anthu 300 osankhika aja. Iwowa anatenga zakudya ndi malipenga a anthuwo. Ndipo misasa ya ankhondo Amidiyani inali kumunsi kwa chigwa.

Onani mutuwo Koperani




Oweruza 7:8
11 Mawu Ofanana  

Ndipo padzakhala tsiku limenelo, lipenga lalikulu lidzaombedwa; ndipo adzafika omwe akadatayika m'dziko la Asiriya, ndi opirikitsidwa a m'dziko la Ejipito; ndipo adzapembedza Yehova m'phiri lopatulika la pa Yerusalemu.


Nena ndi ana a Israele, ndi kuti, Mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku loyamba la mweziwo, muzipumula, ndiko chikumbutso cha kuliza malipenga, msonkhano wopatulika.


Pamenepo uzitumizira lipenga lomveka m'mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku lakhumi la mweziwo; tsiku la chitetezero mutumizire lipenga lifikire m'dziko lanu lonse.


Ndipo pamene mupita kunkhondo m'dziko lanu kuchita nkhondo pa mdani wakusautsa inu, mulize chokweza ndi malipenga; ndipo Yehova Mulungu wanu adzakumbukira inu, nadzakupulumutsani kwa adani anu.


m'kamphindi, m'kuthwanima kwa diso, pa lipenga lotsiriza; pakuti lipenga lidzalira, ndipo akufa adzaukitsidwa osavunda, ndipo ife tidzasandulika.


Ndipo anthu anafuula, naliza mphalasa ansembe; ndipo kunali, pamene anthu anamva kulira kwa mphalasa, anafuula anthu ndi mfuu yaikulu, niligwa linga pomwepo; nakwera anthu kulowa m'mzinda, yense kumaso kwake; nalanda mzindawo.


Ndipo ansembe asanu ndi awiri azinyamula mphalasa zisanu ndi ziwiri zanyanga za nkhosa zamphongo, natsogolere nazo likasa; koma tsiku lachisanu ndi chiwiri mudzizungulira mzindawo kasanu ndi kawiri, ndi ansembe aziliza mphalasazo.


Ndipo kunali, pakufika iye anaomba lipenga ku mapiri a Efuremu; ndi ana a Israele anatsika naye kuchokera kumapiri, nawatsogolera iye.


Pamenepo Amidiyani onse ndi Aamaleke ndi ana a kum'mawa anasonkhana pamodzi naoloka, namanga misasa m'chigwa cha Yezireele.


Ndipo Yehova anati kwa Gideoni, Ndi anthu mazana atatu akukhatira ndidzakupulumutsani, ndi kupereka Amidiyani m'dzanja lako; koma amuke anthu awa onse, yense kumalo kwake.


Ndipo kunali usiku womwewo, kuti Yehova ananena naye, Tauka, tatsikira kumisasa; pakuti ndaipereka m'dzanja lako.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa