Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Oweruza 7:5 - Buku Lopatulika

5 Ndipo anatsikira nao anthu kumadzi; ndipo Yehova anati kwa Gideoni, Aliyense akapiza madzi pa lilime lake, monga akhatira galu, ameneyo amuike pa yekha; momwemo aliyense agwada pakumwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo anatsikira nao anthu kumadzi; ndipo Yehova anati kwa Gideoni, Aliyense akapiza madzi pa lilime lake, monga akhatira galu, ameneyo amuike pa yekha; momwemo aliyense agwada pakumwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Choncho Gideoni adapita nawo anthu aja kumadziko. Ndipo Chauta adamuuza kuti, “Onse amene akhathire madzi pakumwa ndi lilime, monga m'mene amachitira galu, uŵaike paokha. Ndipo onse amene agwade kuti amwe madzi, uŵaikenso paokha.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Choncho Gideoni anatenga anthuwo ndi kupita nawo ku madzi. Kumeneko Yehova anamuwuza kuti, “Amene amwe madzi mokhathira ndi manja ngati galu uwayike pawokha, ndipo amene amwe atagwada pansi uwayikenso pawokha.”

Onani mutuwo Koperani




Oweruza 7:5
4 Mawu Ofanana  

Ndipo Eliya anati kwa iye, Usachita mantha, kachite monga umo wanenamo, koma yamba wandiotcherako kamkate, nubwere nako kwa ine; ndipo utatero udziphikire wekha ndi mwana wako.


Adzamwa kumtsinje wa panjira; chifukwa chake adzaweramutsa mutu wake.


Ndipo Yehova ananena ndi Gideoni, Anthu akali ochuluka; tsikira nao kumadzi, ndipo ndidzakuyesera iwo komweko; ndipo kudzali kuti iye amene ndimnena kwa iwe, Uyo azimuka nawe, yemweyo azimuka nawe; koma aliyense ndimnena kwa iwe, Uyo asamuke nawe, yemweyo asamuke.


Ndi kuwerenga kwa iwo akukhatira, ndi kuika dzanja lao kukamwa kwao, ndiko mazana atatu; koma ena onse anagwada pakumwa madzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa