Oweruza 7:4 - Buku Lopatulika4 Ndipo Yehova ananena ndi Gideoni, Anthu akali ochuluka; tsikira nao kumadzi, ndipo ndidzakuyesera iwo komweko; ndipo kudzali kuti iye amene ndimnena kwa iwe, Uyo azimuka nawe, yemweyo azimuka nawe; koma aliyense ndimnena kwa iwe, Uyo asamuke nawe, yemweyo asamuke. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 Ndipo Yehova ananena ndi Gideoni, Anthu akali ochuluka; tsikira nao kumadzi, ndipo ndidzakuyesera iwo komweko; ndipo kudzali kuti iye amene ndimnena kwa iwe, Uyo azimuka nawe, yemweyo azimuka nawe; koma aliyense ndimnena kwa iwe, Uyo asamuke nawe, yemweyo asamuke. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 Chauta adauzanso Gideoni kuti, “Anthuŵa akundichulukirabe kwambiri. Uŵatenge, upite nawo ku madzi, ndipo ndikaŵayesa ndine m'malo mwako kumeneko. Amene ndikuuze kuti, ‘Uyu apite nao,’ adzapita nao. Ndipo amene ndikuuze kuti, ‘Uyu asapite nao,’ sadzapita nao.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 Koma Yehova anawuza Gideoni kuti, “Anthuwa achulukabe. Uwatenge upite nawo ku mtsinje ndipo ndikawayesa kumeneko mʼmalo mwako. Ndikadzanena kuti, ‘Uyu apite nawe’ adzapita nawe; koma ndikanena kuti ‘Uyu asapite nawe,’ sadzapita nawe.” Onani mutuwo |