Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Oweruza 7:1 - Buku Lopatulika

1 Pamenepo Yerubaala, ndiye Gideoni, ndi anthu onse okhala naye anauka mamawa, namanga misasa pa chitsime cha Harodi, ndi misasa ya Midiyani inali kumpoto kwao, paphiri la More m'chigwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Pamenepo Yerubaala, ndiye Gideoni, ndi anthu onse okhala naye anauka mamawa, namanga misasa pa chitsime cha Harodi, ndi misasa ya Midiyani inali kumpoto kwao, pa phiri la More m'chigwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Choncho Yerubaala (ndiye kuti Gideoni) ndi anthu onse amene anali naye, adadzuka m'mamaŵa nakamanga zithando zankhondo pambali pa kasupe wa ku Harodi. Zithando za Amidiyani zinali m'chigwa kumpoto kwao, pafupi ndi phiri la More.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Yeru-Baala (Gideoni) ndi anthu ake onse anadzuka mʼmamawa nakamanga misasa pambali pa kasupe ku Harodi. Misasa ya Amidiyani inali mʼchigwa kumpoto kwa phiri la More.

Onani mutuwo Koperani




Oweruza 7:1
14 Mawu Ofanana  

Ndipo Abramu anapitirira m'dzikomo kufikira ku malo a Sekemu, kufikira ku mtengo wathundu wa ku More. Akanani anali m'dzikomo nthawi yomweyo.


Ndipo Abrahamu analawira m'mamawa namanga bulu wake, natengako anyamata ake awiri pamodzi naye, ndi Isaki mwana wake, nawaza nkhuni za nsembe yopsereza, nauka, nanka kumalo komwe Mulungu anamuuza iye.


Sama Mharodi, Elika Mharodi;


Muwachitire monga munachitira Midiyani; ndi Sisera, ndi Yabini kumtsinje wa Kisoni,


Chilichonse dzanja lako lichipeza kuchichita, uchichite ndi mphamvu yako; pakuti mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziwa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.


Sakhala kodi tsidya lija la Yordani, m'tseri mwake mwa njira yake yolowa dzuwa, m'dziko la Akanani, akukhala m'chidikha, pandunji pake pa Giligala, pafupi pa mathundu a More?


Ndipo Yoswa analawirira mamawa, kuchoka ku Sitimu, nafika ku Yordani, iye ndi ana onse a Israele; nagona komweko, asanaoloke.


Ndipo Yoswa analawira mamawa, ndi ansembe anasenza likasa la Yehova.


Chifukwa chake anamutcha tsiku lija Yerubaala, ndi kuti, Amnenere mlandu Baala popeza anamgamulira guwa lake la nsembe.


Pamenepo Amidiyani onse ndi Aamaleke ndi ana a kum'mawa anasonkhana pamodzi naoloka, namanga misasa m'chigwa cha Yezireele.


Ndipo Mulungu anatero usiku uja; pakuti panauma pachikopa pokha, ndi panthaka ponse panali mame.


Ndipo Yerubaala, mwana wa Yowasi anamuka, nakhala m'nyumba ya iye yekha.


Ndipo Yehova anatumiza Yerubaala, ndi Baraki, ndi Yefita, ndi Samuele, napulumutsa inu m'manja mwa adani anu pozungulira ponse, ndipo munakhala mosatekeseka.


Tsono Afilisti anasonkhanitsa makamu ao onse ku Afeki; ndipo Aisraele anamanga ku chitsime cha mu Yezireele.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa