Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Oweruza 4:9 - Buku Lopatulika

9 Nati iye, Kumuka ndidzamuka nawe, koma ulendo umukawo, sudzachita nao ulemu; pakuti Yehova adzagulitsa Sisera m'dzanja la mkazi. Motero Debora anauka namuka ndi Baraki ku Kedesi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Nati iye, Kumuka ndidzamuka nawe, koma ulendo umukawo, sudzachita nao ulemu; pakuti Yehova adzagulitsa Sisera m'dzanja la mkazi. Motero Debora anauka namuka ndi Baraki ku Kedesi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Debora adati, “Chabwino, ndipita nanu, komatu inu simudzalandirapo ulemu mutapambana, pakuti Chauta adzapereka Sisera m'manja mwa munthu wamkazi.” Tsono Debora adanyamuka kupita ku Kedesi pamodzi ndi Baraki.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Debora anati, “Chabwino, ine ndipita nawe limodzi. Koma mudziwe kuti inu simudzalandirapo ulemu pa zimene mwachitazi popeza Yehova wapereka Sisera mʼmanja mwa munthu wamkazi.” Choncho Debora ananyamuka kupita ku Kedesi pamodzi ndi Baraki.

Onani mutuwo Koperani




Oweruza 4:9
9 Mawu Ofanana  

natsutsana ndi mfumu Uziya, nati kwa iye, Sikuyenera inu, Uziya, kufukizira Yehova koma ansembe, ana a Aroni opatulidwira kufukiza; tulukani m'malo opatulika; pakuti mwalakwa; Yehova Mulungu sakulemekezanipo.


Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Israele, ndipo anawapereka m'manja a ofunkha kuti awafunkhe; nawagulitsa m'dzanja la adani ao akuwazungulira osakhozanso iwowo kuima pamaso pa adani ao.


Ndipo Baraki anati kwa iye, Ukamuka nane, ndidzamuka; ukapanda kumuka nane, sindimuka.


Ndipo mkazi wina anaponya mwala wa mphero pamutu pa Abimeleki, naphwanya bade lake.


Pamenepo anaitana msanga mnyamata wake wosenza zida zake, nanena naye, Solola lupanga lako nundiphe, angamanenere anthu, ndi kuti, Anamupha ndi mkazi. Nampyoza mnyamata wake, nafa iye.


Chifukwa chake Yehova Mulungu wa Israele akuti, Ndinaterodi kuti banja lako ndi banja la kholo lako lidzayenda pamaso panga nthawi zonse; koma tsopano Yehova ati, Chikhale kutali ndi Ine; popeza amene andilemekeza Ine, Inenso ndidzawalemekeza iwowa, ndipo akundipeputsa Ine, adzapeputsidwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa