Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Oweruza 4:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo Debora, mneneri wamkazi, ndiye mkazi wake wa Lapidoti, anaweruza Israele nyengo ija.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo Debora, mneneri wamkazi, ndiye mkazi wake wa Lapidoti, anaweruza Israele nyengo ija.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Nthaŵi imeneyo Debora mneneri wamkazi, mkazi wa Lapidoti, ndiye amene ankatsogolera Aisraele.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Debora, mneneri wamkazi, mkazi wake wa Rapidoti ndiye ankatsogolera Israeli nthawi imeneyo.

Onani mutuwo Koperani




Oweruza 4:4
13 Mawu Ofanana  

Namuka Hilikiya wansembe, ndi Ahikamu, ndi Akibori, ndi Safani, ndi Asaya, kwa Hulida mneneri wamkazi, ndiye mkazi wa Salumu mwana wa Tikiva, mwana wa Harihasi, wosunga zovala za mfumu; analikukhala iye mu Yerusalemu m'dera lachiwiri, nalankhula naye.


Mukumbukire, Mulungu wanga, Tobiya ndi Sanibalati monga mwa ntchito zao izi, ndi Nowadiya mneneri wamkazi yemwe, ndi aneneri otsala, amene anafuna kundiopsa.


Ndipo Miriyamu mneneriyo, mlongo wa Aroni, anagwira lingaka m'dzanja lake; ndipo akazi onse anatuluka kumtsata ndi malingaka ndi kuthira mang'ombe.


Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, uziika nkhope yako itsutsane nao ana aakazi a anthu ako, akunenera za m'mtima mwao, nunenere chowatsutsa,


Pakuti ndinakukwezani kukutulutsani m'dziko la Ejipito, ndi kuombola inu m'nyumba ya ukapolo; ndipo ndinatuma akutsogolereni Mose, Aroni, ndi Miriyamu.


Ndipo panali Anna, mneneri wamkazi, mwana wa Fanuwele, wa fuko la Asere; amene anali wokalamba ndithu, nakhala ndi mwamuna wake, kuyambira pa unamwali wake,


Ndipo munthuyu anali nao ana aakazi anai, anamwali, amene ananenera.


Koma mkazi yense wakupemphera, kapena kunenera, wovula mutu, anyoza mutu wake; pakuti kuli chimodzimodzi kumetedwa.


Muno mulibe Myuda, kapena Mgriki, muno mulibe kapolo, kapena mfulu, muno mulibe mwamuna ndi mkazi; pakuti muli nonse mmodzi mwa Khristu Yesu.


Ndipo ana a Israele anafuula kwa Yehova; pakuti anali nao magaleta achitsulo mazana asanu ndi anai; napsinja ana a Israele kolimba zaka makumi awiri.


Ndipo anakhala patsinde pa mgwalangwa wa Debora pakati pa Rama ndi Betele ku mapiri a Efuremu; ndi ana a Israele anakwera kwa iye awaweruze.


Ndipo Debora ndi Baraki mwana wa Abinowamu anaimba tsiku lomwelo ndi kuti,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa