Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Oweruza 4:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo Yehova anawagulitsa m'dzanja la Yabini mfumu ya Kanani, wochita ufumu ku Hazori; kazembe wake wa nkhondo ndiye Sisera, wokhala ku Haroseti wa amitundu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo Yehova anawagulitsa m'dzanja la Yabini mfumu ya Kanani, wochita ufumu ku Hazori; kazembe wake wa nkhondo ndiye Sisera, wokhala ku Haroseti wa amitundu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Ndipo Chauta adaŵapereka m'manja mwa Yabini, mfumu ya ku Kanani, amene ankalamulira ku Hazori. Mtsogoleri wa ankhondo ake anali Sisera amene ankakhala ku Haroseti-Goimu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Choncho Yehova anawapereka mʼmanja mwa Yabini, mfumu ya ku Kanaani, imene inkalamulira ku Hazori. Mkulu wa ankhondo ake anali Sisera, amene ankakhala ku Haroseti-Hagoyimu.

Onani mutuwo Koperani




Oweruza 4:2
11 Mawu Ofanana  

Muwachitire monga munachitira Midiyani; ndi Sisera, ndi Yabini kumtsinje wa Kisoni,


Atero Yehova, Kalata ya chilekaniro cha amai ako ali kuti amene ndinamsudzula naye? Pena ndani wa angongole anga amene ndamgulitsa iwe? Taona chifukwa cha zoipa zanu munagulitsidwa, ndi chifukwa cha kulakwa kwanu amanu anachotsedwa.


Koma popeza iye anasowa kanthu kombwezera, mbuye wake analamulira kuti iye agulitsidwe, ndi mkazi wake ndi ana ake omwe, ndi zonse ali nazo, kuti akabwezedwe mangawawo.


Ndipo kunali, pamene Yabini mfumu ya ku Hazori anachimva, anatuma kwa Yobabu mfumu ya ku Madoni, ndi kwa mfumu ya ku Simironi, ndi kwa mfumu ya ku Akisafu,


ndi Adama, ndi Rama, ndi Hazori;


Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Israele, nawagulitsa m'dzanja la Afilisti, ndi m'dzanja la ana a Amoni.


Pamenepo Sisera anasonkhanitsa magaleta ake onse ndiwo magaleta mazana asanu ndi anai achitsulo, ndi anthu onse okhala naye, kuyambira Haroseti wa amitundu mpaka mtsinje wa Kisoni.


Koma Baraki anatsata magaleta ndi gululo mpaka Haroseti wa amitundu; ndi gulu lonse lankhondo la Sisera linagwa ndi lupanga lakuthwa, sanatsale munthu ndi mmodzi yense.


Koma iwowa anaiwala Yehova Mulungu wao, Iye nawapereka m'dzanja la Sisera kazembe wa gulu la Hazori, ndi m'dzanja la Afilisti, ndi m'dzanja la mfumu ya Mowabu, iwo naponyana nao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa