Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Oweruza 3:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo pamene ana a Israele anafuula kwa Yehova, Yehova anaukitsira ana a Israele mpulumutsi amene anawapulumutsa, ndiye Otiniyele mwana wa Kenazi, mng'ono wake wa Kalebe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo pamene ana a Israele anafuula kwa Yehova, Yehova anaukitsira ana a Israele mpulumutsi amene anawapulumutsa, ndiye Otiniyele mwana wa Kenazi, mng'ono wake wa Kalebe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Koma pamene Aisraele adalira kwa Chauta, Chautayo adaŵautsira munthu woŵapulumutsa; amene adaŵapulumutsayo ndi Otiniyele, mwana wa Kenazi, mng'ono wake wa Kalebe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Koma pamene Aisraeliwo analirira kwa Yehova, Iye anawawutsira mpulumutsi, Otanieli mwana wamwamuna wa Kenazi, mngʼono wake wa Kalebe. Iyeyu ndiye anawapulumutsa.

Onani mutuwo Koperani




Oweruza 3:9
15 Mawu Ofanana  

Chifukwa chake munawapereka m'dzanja la adani ao akuwasautsa; koma mu nthawi ya kusautsika kwao anafuula kwa Inu, ndipo munamva mu Mwamba, ndi monga mwa nsoni zanu zambiri munawapatsa apulumutsi akuwapulumutsa m'dzanja la adani ao.


Anafuula kwa Inu, napulumutsidwa; anakhulupirira Inu, ndipo sanachite manyazi.


Pamene anawapha ndipo anamfuna Iye; nabwerera, nafunitsitsa Mulungu.


Ndipo Otiniyele mwana wa Kenazi, mbale wake wa Kalebe, anaulanda; ndipo anampatsa Akisa mwana wake akhale mkazi wake.


Ndipo Otiniyele, mwana wa Kenazi mng'ono wa Kalebe anaulanda, ndipo anampatsa Akisa mwana wake wamkazi akhale mkazi wake.


Ndipo ana a Israele anafuula kwa Yehova ndi kuti, Takuchimwirani, popeza tasiya Mulungu wathu ndi kutumikira Abaala.


Ndipo Yehova anautsa oweruza, amene anawapulumutsa m'dzanja la iwo akuwafunkha.


Ndipo pamene Yehova anawaukitsira oweruza, Yehova anakhala naye woweruzayo, nawapulumutsa m'dzanja la adani ao masiku onse a woweruzayo; pakuti Yehova anagwidwa chisoni pa kubuula kwao chifukwa cha iwo akuwapsinja ndi kuwatsendereza.


Koma pamene ana a Israele anafuula kwa Yehova, Yehova anawaukitsira mpulumutsi, Ehudi mwana wa Gera, Mbenjamini, munthu wamanzere, ndipo ana a Israele anatumiza mtulo m'dzanja lake kwa Egiloni mfumu ya Mowabu.


Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Israele ndipo anawagulitsa m'dzanja la Kusani-Risataimu, mfumu ya Mesopotamiya; ndi ana a Israele anatumikira Kusani-Risataimu zaka zisanu ndi zitatu.


Ndipo ana a Israele anafuula kwa Yehova; pakuti anali nao magaleta achitsulo mazana asanu ndi anai; napsinja ana a Israele kolimba zaka makumi awiri.


Ndipo kunali, pamene ana a Israele anafuula kwa Yehova chifukwa cha Midiyani,


Ndipo anapemphera kwa Yehova, kuti, Tinachimwa, popeza tinasiya Yehova, ndi kutumikira Abaala ndi Asitaroti, koma mutipulumutse tsopano m'manja a adani anthu, ndipo tidzakutumikirani Inu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa