Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Oweruza 2:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo anthuwo anatumikira Yehova masiku onse a Yoswa, ndi masiku onse a akuluakulu otsala atafa Yoswa, amene adaona ntchito yaikulu yonse ya Yehova anaichitira Israele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo anthuwo anatumikira Yehova masiku onse a Yoswa, ndi masiku onse a akuluakulu otsala atafa Yoswa, amene adaona ntchito yaikulu yonse ya Yehova anaichitira Israele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Anthuwo ankatumikira Chauta masiku onse pamene Yoswa anali moyo, ndipo ngakhale atafa Yoswayo, anthu ankatumikirabe Chauta nthaŵi yonse ya moyo wa akuluakulu otsatira Yoswa aja, amene anali ataona ntchito zazikulu zimene Chauta adachitira Aisraele.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Anthuwo anatumikira Yehova masiku onse a moyo wa Yoswa. Atamwalira Yoswa, Aisraeli anatumikirabe Yehova nthawi yonse ya moyo wa akuluakulu amene anaona zazikulu zimene Yehova anawachitira.

Onani mutuwo Koperani




Oweruza 2:7
8 Mawu Ofanana  

Ndipo Yowasi anachita zoongoka pamaso pa Yehova masiku ake onse, m'mene anamlangizira wansembe Yehoyada.


Ndipo Yowasi anachita zoongoka pamaso pa Yehova masiku onse a Yehoyada wansembe.


Potero, okondedwa anga, monga momwe mumvera nthawi zonse, posati pokhapokha pokhala ine ndilipo, komatu makamaka tsopano pokhala ine palibe, gwirani ntchito yake ya chipulumutso chanu ndi mantha, ndi kunthunthumira;


Ndipo Israele anatumikira Yehova masiku onse a Yoswa, ndi masiku onse a akuluakulu otsala atafa Yoswa, amene anadziwa ntchito yonse ya Yehova anaichitira Israele.


Koma sanamvere angakhale oweruza ao, pakuti anamuka kupembedza milungu ina, naigwadira; anapatuka msanga m'njira yoyendamo makolo ao, pomvera malamulo a Yehova; sanatero iwowa.


Pamene Yoswa atawalola anthu amuke, ana a Israele anamuka, yense ku cholowa chake, dziko likhale laolao.


Ndipo Yoswa mwana wa Nuni, mtumiki wa Yehova anafa wa zaka zake zana ndi khumi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa