Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Oweruza 2:5 - Buku Lopatulika

5 Potero analitcha dzina la malowo Bokimu: namphera Yehova nsembe pomwepo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Potero analitcha dzina la malowo Bokimu: namphera Yehova nsembe pomwepo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Malowo adaŵatcha Bokimu (ndiye kuti olira), ndipo adapereka nsembe kwa Chauta pomwepo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 ndipo anatcha malowo kuti Bokimu (kutanthauza kuti Olira). Pamenepo anapereka nsembe kwa Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Oweruza 2:5
8 Mawu Ofanana  

Ndipo anafa Debora mlezi wa Rebeka, naikidwa kunsi kwa Betele, pansi pa mtengo wathundu; ndipo anatcha dzina lake Aloni-Bakuti.


Ndipo anamuunjikira mulu waukulu wamiyala, wokhalako kufikira lero lino; ndipo Yehova anatembenuka kusiya mkwiyo wake waukulu. Chifukwa chake anatcha dzina lake la malowo, Chigwa cha Akori, mpaka lero lino.


Pamenepo Manowa anatenga mwanawambuzi pamodzi ndi nsembe yaufa, nazipereka kwa Yehova pathanthwe; ndipo mthengayo anachita modabwitsa, ndi Manowa ndi mkazi wake ali chipenyere.


Ndipo mthenga wa Yehova anakwera kuchokera ku Giligala kunka ku Bokimu. Ndipo anati, Ndinakukweretsani kuchokera ku Ejipito, ndi kulowetsa inu m'dziko limene ndinalumbirira makolo anu; ndipo ndinati, Sindidzathyola chipangano changa nanu ku nthawi yonse;


Ndipo kunali, pamene mthenga wa Yehova ananena mau awa kwa ana onse a Israele, anthuwo anakweza mau ao, nalira misozi.


Pamene Yoswa atawalola anthu amuke, ana a Israele anamuka, yense ku cholowa chake, dziko likhale laolao.


Pamenepo Gideoni anammangira Yehova guwa la nsembe pomwepo; nalitcha Yehova-ndiye-mtendere; likali mu Ofura wa Aabiyezere ndi pano pomwe.


Ndipo Samuele anatenga mwanawankhosa woyamwa, nampereka wathunthu kwa Yehova, nsembe yopsereza; ndipo Samuele anapempherera Israele kwa Yehova; ndipo Yehova anamvomereza.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa