Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Oweruza 2:3 - Buku Lopatulika

3 Chifukwa chakenso ndinati, Sindidzawapirikitsa kuwachotsa pamaso panu; koma adzakhala ngati minga m'nthiti zanu, ndi milungu yao idzakhalira inu msampha.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Chifukwa chakenso ndinati, Sindidzawapirikitsa kuwachotsa pamaso panu; koma adzakhala ngati minga m'nthiti zanu, ndi milungu yao idzakhalira inu msampha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Choncho tsopano ndikukuuzani kuti sindidzapirikitsa nzikazo pamene inu mukufika. Koma zidzasanduka adani anu, ndipo milungu yao idzakhala ngati msampha kwa inu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Ndikukuwuzani tsopano kuti sindithamangitsa nzikazo pamene inu mukufika. Ndidzawasandutsa kukhala adani anu ndipo milungu yawo idzakhala ngati msampha kwa inu.”

Onani mutuwo Koperani




Oweruza 2:3
11 Mawu Ofanana  

Ndipo anatumikira mafano ao, amene anawakhalira msampha:


Asakhale m'dziko lako iwowa, kuti angakulakwitse pa Ine; pakuti ukatumikira milungu yao, kudzakukhalira msampha ndithu.


Dzichenjere ungachite pangano ndi anthu a ku dziko limene umukako, lingakhale msampha pakati panu;


Koma mukapanda kupirikitsa okhala m'dziko pamaso panu, pamenepo iwo amene muwalola atsale adzakhala ngati zotwikira m'maso mwanu, ndi minga m'mbali zanu, nadzakuvutani m'dziko limene mukhalamo.


Ndipo mudzatha mitundu yonse ya anthu amene Yehova Mulungu wanu adzapereka kwa inu; diso lanu lisawachitire chifundo; musamatumikira milungu yao; pakuti uku kudzakuchitirani msampha.


dziwani ndithu kuti Yehova Mulungu wanu sadzalandanso dziko la amitundu awa kuwachotsa pamaso panu; koma adzakhala kwa inu deka ndi msampha ndi mkwapulo m'nthiti mwanu, ndi minga m'maso mwanu, mpaka mudzatayika m'dziko lokoma ili anakupatsani Yehova Mulungu wanu.


Inenso sindionjeza kuingitsa pamaso pao a mitundu ina imene Yoswa adaisiya pakufa iyeyu;


Ndipo kunali, pamene mthenga wa Yehova ananena mau awa kwa ana onse a Israele, anthuwo anakweza mau ao, nalira misozi.


nakwatira ana aakazi a iwowa, napereka ana ao akazi kwa ana aamuna a iwowa natumikira milungu yao.


Ndipo Gideoni anawapanga fano, naliika m'mzinda mwake, ndiwo Ofura; ndi Israele yense analitsata kuligwadira pomwepo; ndipo linakhala kwa Gideoni ndi nyumba yake ngati msampha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa