Oweruza 17:4 - Buku Lopatulika4 Ndipo pamene anambwezera mai wake ndalamazo, mai wake anatapako ndalama mazana awiri, nazipereka kwa woyenga, ndiye anazipanga fano losema ndi fano loyenga; ndipo linakhala m'nyumba ya Mika. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 Ndipo pamene anambwezera mai wake ndalamazo, mai wake anatapako ndalama mazana awiri, nazipereka kwa woyenga, ndiye anazipanga fano losema ndi fano loyenga; ndipo linakhala m'nyumba ya Mika. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 Tsono Mika atabweza ndalamazo kwa mai wake, mai wakeyo adatengapo ndalama zasiliva 200 nazipereka kwa mmisiri wosula siliva. Munthuyo adasema fano nasungunula ndalamazo, nakutira fanolo ndi siliva. Ndipo Mika adaliimika m'nyumba mwake. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 Tsono Mika atabweza ndalama zija kwa amayi ake, iwo anatengapo ndalama za siliva 200 namupatsa mmisiri wosula siliva. Iye anakonza fano, nasungunula siliva uja ndi kulikutira fano lija. Ndipo Mika anayika fanolo mʼnyumba mwake. Onani mutuwo |