Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Oweruza 17:3 - Buku Lopatulika

3 Nabwezera amake ndalama zija mazana khumi ndi limodzi; nati amai wake, Kupatula ndapatulira Yehova ndalamazo zichoke ku dzanja langa, zimuke kwa mwana wanga, kupanga nazo fano losema ndi fano loyenga; m'mwemo ndikubwezera izi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Nabwezera amake ndalama zija mazana khumi ndi limodzi; nati amai wake, Kupatula ndapatulira Yehova ndalamazo zichoke ku dzanja langa, zimuke kwa mwana wanga, kupanga nazo fano losema ndi fano loyenga; m'mwemo ndikubwezera izi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Tsono iye adabwezera ndalama zonse kwa mai wake, ndipo maiyo pofuna kuchotsa temberero lija, adati, “Ndikuzipatula ndalama zasilivazi kuti zikhale za Chauta. Ndidzazipereka kuti aseme fano ndi kulikuta ndi siliva. Choncho ndikubwezera ndalamazo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Choncho Mika anabweza ndalama 1,100 za siliva kwa amayi ake, ndipo amayi akewo anati, “Ine ndapatulira Yehova ndalama za silivazi kuti mwana wanga aseme fano ndi kulikuta ndi siliva. Ndiye tsopano ndikubwezera ndalamazo.”

Onani mutuwo Koperani




Oweruza 17:3
21 Mawu Ofanana  

Ndipo anaika chifanizo chosema cha fanolo adachipanga m'nyumba ya Mulungu, imene Mulungu adati kwa Davide ndi Solomoni mwana wake, M'nyumba muno ndi mu Yerusalemu umene ndausankha m'mafuko onse a Israele ndidzaika dzina langa kunthawi zonse;


Musapange milungu yasiliva ikhale pamodzi ndi Ine; musadzipangire milungu yagolide.


Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena chifaniziro chilichonse cha zinthu za m'thambo la kumwamba, kapena za m'dziko lapansi, kapena za m'madzi a pansi padziko.


Usadzipangire milungu yoyenga.


Ndipo mudzaipitsa chokuta cha mafano ako, osema asiliva, ndi chomata cha mafano ako osungunula agolide; udzawataya ngati kanthu konyansa, udzati kwa iwo, Chokani.


Wakupha ng'ombe alingana ndi wakupha munthu; iye wapereka nsembe ya mwanawankhosa alingana ndi wothyola khosi la galu; wothira nsembe yaufa akunga wothira mwazi wa nkhumba; wofukiza lubani akunga wodalitsa fano; inde iwo asankha njira zaozao, ndipo moyo wao ukondwerera m'zonyansa zao;


Koma onse pamodzi apulukira ndi kupusa; mtengo ndiwo chilangizo, chopanda pake.


Musamatembenukira mafano, kapena kudzipangira mulungu woyenga; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.


Adzakutulutsani m'masunagoge, koma ikudza nthawi imene yense wakupha inu adzayesa kuti atumikira Mulungu.


nimugumule maguwa ao a nsembe, ndi kuphwanya zoimiritsa zao, ndi kutentha zifanizo zao, ndi kulikha mafano osema a milungu yao; ndipo muononge dzina lao lichoke m'malomo.


Wotembereredwa munthu wakupanga fano losema kapena loyenga, lonyansidwa nalo Yehova, ntchito ya manja a mmisiri, ndi kuliika m'malo a m'tseri. Ndipo anthu onse ayankhe ndi kuti, Amen.


Nati Mika, Tsopano ndidziwa kuti Yehova adzandichitira chokoma, popeza ndili naye Mlevi akhale wansembe wanga.


Ndipo iye anati kwa amai wake, Ndalama zija mazana khumi ndi limodzi anakuberani zimene munatembererapo, ndi kunenanso m'makutu mwanga, taonani ndalamazo ndili nazo, ndinazitenga ndine. Pamenepo amai wake anati, Yehova adalitse mwana wanga.


Ndipo pamene anambwezera mai wake ndalamazo, mai wake anatapako ndalama mazana awiri, nazipereka kwa woyenga, ndiye anazipanga fano losema ndi fano loyenga; ndipo linakhala m'nyumba ya Mika.


Ndipo ana a Dani anadziimitsira fano losemalo; ndi Yonatani mwana wa Geresomo mwana wa Manase, iye ndi ana ake aamuna anali ansembe a fuko la Adani mpaka tsiku lija anatenga ndende anthu a m'dziko.


Pamenepo ananena naye, Utifunsire kwa Mulungu, kuti tidziwe ngati ulendo wathu timukawo udzakoma.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa