Oweruza 16:9 - Buku Lopatulika9 Koma anali nao omlalira m'chipinda cha m'kati. Nanena naye, Afilisti akugwera, Samisoni. Pamenepo anadula nsingazi, monga iduka m'khosi yathonje pokhudza moto. M'mwemo mphamvu yake siinadziwike. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Koma anali nao omlalira m'chipinda cha m'kati. Nanena naye, Afilisti akugwera, Samisoni. Pamenepo anadula nsingazi, monga iduka m'khosi yathonje pokhudza moto. M'mwemo mphamvu yake siinadziwike. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 Nthaŵi imeneyo nkuti mkaziyo ataika anthu ombisalirawo m'chipinda cham'kati. Kenaka adafuula kwa mwamuna wake kuti, “Inu amuna anga, Afilisti aja akubwera.” Koma iye adangomwetula nsingazo monga m'mene imamwetukira nkhosi ya chingwe ikamapsa. Choncho chinsinsi cha mphamvu zakezo sichidadziŵikebe. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Nthawi imeneyo nʼkuti mkazi uja atayika anthu omubisalira mʼchipinda. Tsono anati kwa mwamuna wake, “Amuna anga, Afilisti aja afika!” Koma iye anangodula zingwe zija ngati mmene imadukira nkhosi ya chingwe ikamapsa. Choncho chinsinsi cha mphamvu zake sichinadziwike. Onani mutuwo |