Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Oweruza 16:7 - Buku Lopatulika

7 Nanena naye Samisoni, Akandimanga nazo nsinga zatsopano zisanu ndi ziwiri zosauma, ndidzakhala wofooka, wakunga munthu wina.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Nanena naye Samisoni, Akandimanga nazo nsinga zatsopano zisanu ndi ziwiri zosauma, ndidzakhala wofooka, wakunga munthu wina.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Samisoni adamuuza kuti, “Atandimanga ndi nsinga zatsopano zisanu ndi ziŵiri zosauma, ndidzasanduka wofooka ndipo ndidzafanafana ndi munthu wina aliyense.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Samsoni anamuyankha kuti, “Ngati wina atandimanga ndi zingwe zisanu ndi ziwiri zatsopano zosawuma, ndidzafowoka ndi kusanduka ngati munthu wina aliyense.”

Onani mutuwo Koperani




Oweruza 16:7
12 Mawu Ofanana  

Mlomo wa ntheradi ukhazikika nthawi zonse; koma lilime lonama likhala kamphindi.


Mlomo wangwiro suyenera chitsiru; ngakhale mlomo wonama suyenera kalonga ndi pang'ono ponse.


Ndipo tilekerenji kunena, Tichite zoipa kuti zabwino zikadze (monganso ena atinamiza ndi kuti timanena)? Kulanga kwa amenewo kuli kolungama.


Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta.


musamanamizana wina ndi mnzake; popeza mudavula munthu wakale pamodzi ndi ntchito zake,


Pamenepo Delila anati kwa Samisoni, Taona, wandipusitsa, ndi kundiuza mabodza; undiuze tsopano, ndikupempha, chimene angakumange nacho.


Pamenepo Delila anati kwa Samisoni, Ndikupempha, undiuze umo muchokera mphamvu yako yaikulu, ndi chimene angakumange nacho, kuti akuzunze.


Pamenepo akalonga a Afilisti anakwera nazo kwa mkaziyo nsinga zatsopano zisanu ndi ziwiri zosauma; ndipo iye anammanga nazo.


Koma anali nao omlalira m'chipinda cha m'kati. Nanena naye, Afilisti akugwera, Samisoni. Pamenepo anadula nsingazi, monga iduka m'khosi yathonje pokhudza moto. M'mwemo mphamvu yake siinadziwike.


Nati Saulo kwa Mikala, Wandinyengeranji chomwechi, ndi kulola mdani wanga apulumuke? Ndipo Mikala anayankha Saulo, Iye anati kwa ine, Undilole ndipite, ndingakuphe.


Ndipo Akisi anati, Waponyana nkhondo ndi yani lero? Nati Davide, Ndi a kumwera kwa Ayuda, ndi a kumwera kwa Ayerameele, ndi a kumwera kwa Akeni.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa