Oweruza 16:3 - Buku Lopatulika3 Koma Samisoni anagona mpaka pakati pa usiku, nauka pakati pa usiku, nagwira zitseko za pa chipata cha mzinda, ndi mphuthu ziwirizo, nazichotsa ndi mpiringidzo womwe, naziika pa mapewa ake, nakwera nazo pamwamba paphiri lili pandunji pa Hebroni. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Koma Samisoni anagona mpaka pakati pa usiku, nauka pakati pa usiku, nagwira zitseko za pa chipata cha mudzi, ndi mphuthu ziwirizo, nazichotsa ndi mpiringidzo womwe, naziika pa mapewa ake, nakwera nazo pamwamba pa phiri lili pandunji pa Hebroni. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Koma Samisoni adagona mpaka pakati pa usiku. Pakati pa usikupo adadzuka, nagwira zitseko zapachipata ndi mafuremu ake onse aŵiri. Adazizula pamodzi ndi mpiringidzo ndi zina zonse. Adazisenza pa phewa, napita nazo pamwamba pa phiri loyang'anana ndi Hebroni. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Koma Samsoni anangogonako mpaka pakati pa usiku. Kenaka pakati pa usiku anadzuka nagwira zitseko za chipata cha mzinda ndi maferemu ake awiri, ndipo anazizula zonse pamodzi ndi mpiringidzo womwe. Anazisenza pa mapewa pake napita nazo pamwamba pa phiri loyangʼanana ndi Hebroni. Onani mutuwo |