Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Oweruza 15:5 - Buku Lopatulika

5 Nayatsa miuni, nawataya ku tirigu wosacheka wa Afilisti, natentha miulu, ndi tirigu wosacheka yemwe, ndi minda ya azitona yomwe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Nayatsa miuni, nawataya ku tirigu wosacheka wa Afilisti, natentha miulu, ndi tirigu wosacheka yemwe, ndi minda ya azitona yomwe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Atayatsa nsakalizo, adazitaya nkhandwezo kuti zipite m'minda yatirigu ya Afilisti. Popitapo zidakatentha milu ya tirigu ndi tirigu wosadula yemwe, pamodzi ndi mitengo ya olivi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Anayatsa nsakalizo kenaka ndi kuzitayira nkhandwe zija mʼminda ya tirigu ya Afilisti, ndipo zinatentha milu ya tirigu, ndi wosadula yemwe pamodzi ndi mitengo ya mpesa ndi ya olivi.

Onani mutuwo Koperani




Oweruza 15:5
5 Mawu Ofanana  

Chifukwa chake iye anati kwa anyamata ake, Onani munda wa Yowabu uli pafupi ndi wanga, ndipo iye ali ndi barele pamenepo, mukani mukamtenthere. Ndipo anyamata a Abisalomu anatentha za m'mundawo.


Ukayaka moto, nukalandira kuminga, kotero kuti unyeketsa mulu wa tirigu, kapena tirigu wosasenga, kapena munda; woyatsa motoyo alipe ndithu.


koma chaka chachisanu ndi chiwiri uuleke, ugone; kuti aumphawi a anthu a mtundu wako adyemo, ndipo zotsalira nyama zakuthengo zizidye; momwemo uzichita ndi munda wako wampesa, ndi munda wako wa azitona.


Namuka Samisoni, nagwira ankhandwe mazana atatu, natenga miuni, nalunza michira, naika muuni pakati pa michira iwiri iliyonse.


Pamenepo Afilisti anati, Wachita ichi ndani? Nati, Samisoni mkamwini wa munthuyo wa ku Timna, popeza analanda mkazi wake, nampereka kwa mnzake. Pamenepo Afilisti anakwera namtentha mkaziyo ndi atate wake ndi moto.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa