Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Oweruza 13:8 - Buku Lopatulika

8 Pamenepo Manowa anapembedza Yehova, nati, Yehova, ndikupemphani, atidzerenso munthu wa Mulungu mudamtumayo, natilangize icho tizichitira mwanayo akadzabadwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Pamenepo Manowa anapembedza Yehova, nati, Yehova, ndikupemphani, atidzerenso munthu wa Mulungu mudamtumayo, natilangize icho tizichitira mwanayo akadzabadwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Tsono Manowa adapemphera kwa Chauta kuti, “Inu Chauta, ndapota nanu, mulole kuti munthu amene mudaamtuma uja abwerenso, adzatiphunzitse zimene tiyenera kuchita naye mnyamata amene adzabadweyo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Kenaka Manowa anapemphera kwa Yehova kuti, “Chonde Ambuye, lolani munthu wa Mulungu amene munamutuma abwerenso kwa ife kuti adzatiphunzitse zochita ndi mwanayo akadzabadwa.”

Onani mutuwo Koperani




Oweruza 13:8
8 Mawu Ofanana  

Chimene sindichiona mundilangize ndi Inu, ngati ndachita chosalungama sindidzabwerezanso.


komatu, uka, nulowe m'mzinda, ndipo kudzanenedwa kwa iwe chimene uyenera kuchita.


Nanyamuka Manowa natsata mkazi wake, namdzera mwamuna uja, nanena naye, Kodi ndinu mwamuna uja munalankhula ndi mkaziyu? Ndipo anati, Ndine amene.


Ndipo mthenga wa Yehova anamuonekera mkaziyo nanena naye, Taona tsopano, ulibe mwana wosabala iwe; koma udzaima ndi kubala mwana wamwamuna.


Pamenepo anadza mkaziyo, nanena ndi mwamuna wake ndi kuti, Wandidzera munthu wa Mulungu; maonekedwe ake ndiwo ngati maonekedwe a mthenga wa Mulungu oopsa ndithu; ndipo sindinamfunse uko achokera kapena sanandiuzenso dzina lake;


koma anati kwa ine, Taona, udzaima, ndi kubala mwana wamwamuna; ndipo tsopano usamwe vinyo kapena choledzeretsa, nusadye chilichonse chodetsa; pakuti mwanayo adzakhalira kwa Mulungu Mnaziri chibadwire mpaka tsiku la kufa kwake.


Ndipo Mulungu anamvera mau a Manowa; ndi mthenga wa Mulungu anamdzeranso mkaziyo, pamene anali m'munda, mwamuna wake Manowa palibe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa