Oweruza 12:3 - Buku Lopatulika3 Ndipo pakuona ine kuti simundipulumutsa, ndinataya moyo wanga ndi kupita kwa ana a Amoni; ndipo Yehova anawapereka m'dzanja langa; mwakwereranji tsono lero lino kundichitira nkhondo? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Ndipo pakuona ine kuti simundipulumutsa, ndinataya moyo wanga ndi kupita kwa ana a Amoni; ndipo Yehova anawapereka m'dzanja langa; mwakwereranji tsono lero lino kundichitira nkhondo? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Ndipo nditaona kuti simunkafuna kundipulumutsa, ndidangochita utotomoyo nkuwoloka Yordani kukalimbana nawo Aamoni. Chauta adatithandiza kuŵagonjetsa. Chifukwa chiyani tsono mwabwera kwa ine lero lino kuti mudzachite nane nkhondo?” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Nditaona kuti simundithandiza, ndinayika moyo wanga pa chiswe ndipo ndinawoloka kukachita nkhondo ndi a Aamoni. Yehova anandithandiza ndipo ndinawagonjetsa. Nanga nʼchifukwa chiyani mwabwera kwa ine lero kuti muchite nane nkhondo?” Onani mutuwo |