Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Oweruza 11:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo akulu a Giliyadi ananena ndi Yefita, Chifukwa chake chakuti takubwerera tsopano ndicho kuti umuke nafe ndi kuchita nkhondo ndi ana a Amoni, nudzakhala mkulu wathu wa pa onse okhala mu Giliyadi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo akulu a Giliyadi ananena ndi Yefita, Chifukwa chake chakuti takubwerera tsopano ndicho kuti umuke nafe ndi kuchita nkhondo ndi ana a Amoni, nudzakhala mkulu wathu wa pa onse okhala m'Giliyadi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Apo akuluakuluwo adamuyankha Yefita kuti, “Nchimene tabwerera kwa iwe tsopano lino, kuti upite nafe kukamenyana ndi Aamoni, ndipo ukhale mtsogoleri wathu wolamulira anthu onse a ku Giliyadi.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Akuluakulu a ku Giliyadi aja anamuyankha kuti, “Chimene tabwerera kwa iwe ndi chakuti upite nafe kukamenyana ndi Aamoni, ndipo udzakhala wolamulira wa onse okhala mu Giliyadi.”

Onani mutuwo Koperani




Oweruza 11:8
8 Mawu Ofanana  

Ndipo mfumu inayankha niti kwa munthu wa Mulungu, Undipembedzere Yehova Mulungu wako, nundipempherere, kuti dzanja langa libwerenso kwa ine. Ndipo munthuyo wa Mulungu anapembedza Yehova, ndipo dzanja la mfumu linabwezedwa kwa iye momwemo mwa kale.


Ndipo tsopano, ndikhululukiretu kulakwa kwanga nthawi ino yokha, nimundipembere kwa Yehova Mulungu wanu, kuti andichotsere imfa ino yokha.


Ndipo Farao anati, Ndidzakulolani mumuke, kuti mukamphere nsembe Yehova Mulungu wanu m'chipululu; komatu musamuke kutalitu: mundipembere.


Pamenepo Farao anaitana Mose ndi Aroni, nati, Mundipembere Yehova, kuti andichotsere ine ndi anthu anga achulewo; ndipo ndidzalola anthu amuke, kuti amphere Yehova nsembe.


Pembani kwa Yehova; chifukwa akwanira ndithu mabingu a Mulungu ndi matalala; ndipo ndidzakulolani mumuke, osakhalanso.


Ndipo anthu, akalonga a Giliyadi, ananenana wina ndi mnzake, Ndaniyo adzayamba kulimbana ndi ana a Amoni? Iye adzakhala mkulu wa onse okhala mu Giliyadi.


Ndipo Yefita anati kwa akulu a Giliyadi, Mukandifikitsanso kwathu kuchita nkhondo ndi ana a Amoni, nakawapereka Yehova pamaso panga, ndidzakhala mkulu wanu kodi?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa