Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Oweruza 11:3 - Buku Lopatulika

3 Pamenepo Yefita anathawa abale ake, nakhala m'dziko la Tobu; ndipo anyamata opanda pake anasonkhana kwa Yefita, natuluka naye pamodzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Pamenepo Yefita anathawa abale ake, nakhala m'dziko la Tobu; ndipo anyamata opanda pake anasonkhana kwa Yefita, natuluka naye pamodzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Choncho Yefita adaŵathaŵa abale akewo nakakhala m'dziko la Tobu. Kumeneko adakakopa anzake achabechabe kuti azimtsata ndi kunka nasakaza zinthu pamodzi naye.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Choncho Yefita anathawa kuchoka kwa abale ake ndi kukakhala mʼdziko la Tobu. Kumeneko anakakopa ndi kusonkhanitsa anthu achabechabe ndipo anatuluka pamodzi kukasakaza zinthu.

Onani mutuwo Koperani




Oweruza 11:3
9 Mawu Ofanana  

Ndipo pamene ana a Amoni anazindikira kuti anadzinunkhitsa kwa Davide, ana a Amoniwo anatumiza nadzilembera Aaramu a ku Beterehobu, ndi Aaramu a ku Zoba, oyenda pansi zikwi makumi awiri, ndi mfumu ya ku Maaka ndi anthu chikwi chimodzi, ndi anthu a mfumu ya ku Tobu zikwi khumi ndi ziwiri.


Ndipo ana a Amoni anatuluka, nandandalitsa nkhondo polowera kuchipata. Ndipo Aaramu a ku Zoba ndi a ku Rehobu, ndi anthu a Tobu ndi Maaka, anali pa okha kuthengo.


Koma Ayuda anadukidwa mtima, natenga anthu ena oipa achabe a pabwalo, nasonkhanitsa khamu la anthu, nachititsa phokoso m'mzinda; ndipo anagumukira kunyumba ya Yasoni, nafuna kuwatulutsira kwa anthu.


Ndipo mkazi wa Giliyadi anambalira ana aamuna; koma atakula ana aamuna a mkaziyo anampirikitsa Yefita, nanena naye, Sudzalandira cholowa m'nyumba ya atate wako; pakuti ndiwe mwana wa mkazi wina.


Ndipo anampatsa ndalama makumi asanu ndi awiri za m'nyumba ya Baala-Beriti; ndipo Abimeleki analembera nazo anthu opanda pake ndi opepuka amene anamtsata.


Ndipo yense wosautsidwa, ndi yense wa ngongole, ndi yense wowawidwa mtima, anaunjikana kwa iye; iye nakhala mtsogoleri wao; ndipo anali nao anthu ngati mazana anai.


Ndipo Davide ananyamuka, naoloka pamodzi ndi anthu mazana asanu ndi limodzi amene anali naye, nafika kwa Akisi mwana wa Maoki, mfumu ya ku Gati.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa