Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Oweruza 11:1 - Buku Lopatulika

1 Yefita Mgiliyadi ndipo anali ngwazi yamphamvu, ndiye mwana wa mkazi wadama; koma Giliyadi adabala Yefita.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Yefita Mgiliyadi ndipo anali ngwazi yamphamvu, ndiye mwana wa mkazi wadama; koma Giliyadi adabala Yefita.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Yefita wa ku Giliyadi anali wankhondo wamphamvu. Bambo wake anali Giliyadi, mai wake anali mkazi wadama.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Yefita wa ku Giliyadi anali wankhondo wa mphamvu. Iyeyu amayi ake anali mkazi wachiwerewere, ndipo abambo ake anali Giliyadi.

Onani mutuwo Koperani




Oweruza 11:1
6 Mawu Ofanana  

Ndipo Naamani kazembe wa khamu la nkhondo la mfumu ya Aramu anali munthu womveka pamaso pa mbuyake, ndi waulemu; popeza mwa iye Yehova adapulumutsa Aaramu; ndiyenso ngwazi, koma wakhate.


Ndipo ndinene chiyaninso? Pakuti idzandiperewera nthawi ndifotokozere za Gideoni, Baraki, Samisoni, Yefita; za Davide, ndi Samuele ndi aneneri;


Ndipo anthu, akalonga a Giliyadi, ananenana wina ndi mnzake, Ndaniyo adzayamba kulimbana ndi ana a Amoni? Iye adzakhala mkulu wa onse okhala mu Giliyadi.


Ndipo mkazi wa Giliyadi anambalira ana aamuna; koma atakula ana aamuna a mkaziyo anampirikitsa Yefita, nanena naye, Sudzalandira cholowa m'nyumba ya atate wako; pakuti ndiwe mwana wa mkazi wina.


Ndipo mthenga wa Yehova anamuonekera, nati kwa iye, Yehova ali nawe, ngwazi iwe, wamphamvu iwe.


Ndipo Yehova anatumiza Yerubaala, ndi Baraki, ndi Yefita, ndi Samuele, napulumutsa inu m'manja mwa adani anu pozungulira ponse, ndipo munakhala mosatekeseka.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa