Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Oweruza 10:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo ana a Amoni anaoloka Yordani kuthiranso nkhondo Yuda ndi Benjamini, ndi nyumba ya Efuremu; napsinjika kwambiri Israele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo ana a Amoni anaoloka Yordani kuthiranso nkhondo Yuda ndi Benjamini, ndi nyumba ya Efuremu; napsinjika kwambiri Israele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Ndipo Aamoni adaoloka mtsinje wa Yordani kukamenyana nkhondo ndi fuko la Yuda, la Benjamini ndiponso la Efuremu, kotero kuti Aisraele adazunzika kwambiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Aamori anawoloka mtsinje wa Yorodani kukathira nkhondo mafuko a Yuda, Benjamini ndi Efereimu kotero kuti Israeli anavutika kwambiri.

Onani mutuwo Koperani




Oweruza 10:9
13 Mawu Ofanana  

Ndipo anawatulukira Zera Mkusi ndi ankhondo zikwi chikwi chimodzi, ndi magaleta mazana atatu; nafika iye ku Maresa.


Ndipo nthawi zija panalibe mtendere kwa iye wakutuluka, kapena kwa iye wakulowa, koma mavuto aakulu anagwera onse okhala m'maikomo.


Ndipo mwa a mitundu iyi simudzapumula, inde sipadzakhala popumulira phazi lanu; koma Yehova adzakupatsani kumeneko mtima wonjenjemera, m'maso mwanu mudzada, mudzafa ndi kulefuka mtima.


Ndipo ana a Israele anafuula kwa Yehova ndi kuti, Takuchimwirani, popeza tasiya Mulungu wathu ndi kutumikira Abaala.


Ndipo anaphwanya napsinja ana a Israele chaka chija, natero ndi ana onse a Israele okhala tsidya lija la Yordani m'dziko la Aamori, ndilo Giliyadi, zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu.


Ndipo kunali, atapita masiku, ana a Amoni anachita nkhondo ndi Israele,


Kuli konse anatuluka, dzanja la Yehova linawakhalira moipa, monga Yehova adanena, ndi monga Yehova adawalumbirira; nasautsika kwambiri iwowa.


Pamene dzanja la Midiyani linagonjetsa Israele, ana a Israele anadzikonzera ming'ang'ala ya m'mapiri, ndi mapanga, ndi malinga chifukwa cha Midiyani.


Pamene anthu a Israele anazindikira kuti ali m'kupsinjika, pakuti anthuwo anasauka mtima, anthuwo anabisala m'mapanga, ndi m'nkhalango, ndi m'matanthwe, ndi m'malinga, ndi m'maenje.


Ndipo Samuele ananena ndi Saulo, Wandivutiranji kundikweretsa kuno? Saulo nayankha, Ndilikusautsika kwambiri, pakuti Afilisti aponyana nkhondo ndi ine, ndipo Mulungu anandichokera, osandiyankhanso, kapena ndi aneneri, kapena ndi maloto; chifukwa chake ndakuitanani, kuti mundidziwitse chimene ndiyenera kuchita.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa