Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Oweruza 10:1 - Buku Lopatulika

1 Atafa Abimeleki, anauka kupulumutsa Israele Tola mwana wa Puwa, mwana wa Dodo munthu wa Isakara; nakhala iye mu Samiri ku mapiri a Efuremu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Atafa Abimeleki, anauka kupulumutsa Israele Tola mwana wa Puwa, mwana wa Dodo munthu wa Isakara; nakhala iye m'Samiri ku mapiri a Efuremu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Atafa Abimeleki, padabwera winanso wodzapulumutsa Aisraele. Iyeyu anali Tola, mwana wa Puwa, mdzukulu wa Dodo, wa fuko la Isakara. Ankakhala ku Samiri, m'dziko lamapiri la Efuremu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Atafa Abimeleki panabwera Tola mwana wa Puwa, mdzukulu wa Dodo kudzapulumutsa Aisraeli. Iyeyu anali wa fuko la Isakara ndipo ankakhala ku Samiri mʼdziko la mapiri la Efereimu.

Onani mutuwo Koperani




Oweruza 10:1
8 Mawu Ofanana  

Ndi ana aamuna a Isakara: Tola ndi Puva, ndi Iyobu, ndi Simironi.


Ndi kumapiri Samiri, ndi Yatiri, ndi Soko;


Ndipo anaweruza Israele zaka makumi awiri ndi zitatu, nafa, naikidwa mu Samiri.


Ndi pambuyo pake Ibizani wa ku Betelehemu anaweruza Israele.


Ndipo Yehova anautsa oweruza, amene anawapulumutsa m'dzanja la iwo akuwafunkha.


Ndipo kunali, pakufika iye anaomba lipenga ku mapiri a Efuremu; ndi ana a Israele anatsika naye kuchokera kumapiri, nawatsogolera iye.


Ndipo pamene ana a Israele anafuula kwa Yehova, Yehova anaukitsira ana a Israele mpulumutsi amene anawapulumutsa, ndiye Otiniyele mwana wa Kenazi, mng'ono wake wa Kalebe.


Ndipo Mulungu anawabwezera choipa chonse cha amuna a ku Sekemu pamitu pao, ndipo linawagwera temberero la Yotamu mwana wa Yerubaala.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa