Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 35:30 - Buku Lopatulika

30 Aliyense wakantha munthu, wakupha munthuyo aziphedwa pakamwa pa mboni; koma mboni ya munthu mmodzi isafikire kuti munthu afe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

30 Aliyense wakantha munthu, wakupha munthuyo aziphedwa pakamwa pa mboni; koma mboni ya munthu mmodzi isafikire kuti munthu afe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

30 Ngati wina aliyense apha mnzake, wopha mnzakeyo ayenera kuphedwa, mboni zitapereka umboni wao. Koma munthu asaphedwe pamene munthu mmodzi yekha wapereka umboni.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

30 “ ‘Aliyense wopha munthu ayeneranso kuphedwa ngati pali umboni okwanira. Koma wina asaphedwe ngati pali mboni imodzi yokha.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 35:30
14 Mawu Ofanana  

Iye amene akantha munthu kotero kuti wafa, aphedwe ndithu.


Munthu akakantha munthu mnzake aliyense kuti afe, amuphe ndithu.


Koma akamkantha ndi chipangizo chachitsulo, kuti wafa, ndiye wakupha munthu; wakupha munthu nayenso amuphe ndithu.


Musamalandira dipo lakuombola moyo wa iye adapha munthu, napalamula imfa; koma aziphedwa ndithu.


Koma ngati samvera, onjeza kutenga ndi iwe wina mmodzi kapena awiri, kuti atsimikizidwe mau onse pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu.


Kodi chilamulo chathu chiweruza munthu, osayamba kumva iye, ndi kuzindikira chimene achita?


Nthawi yachitatu iyi ndilinkudza kwa inu. Pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu maneno onse adzakhazikika.


Mboni imodzi isamaukira munthu pa mphulupulu iliyonse, kapena tchimo lililonse adalichimwa; pakamwa pa mboni ziwiri, kapena pakamwa pa mboni zitatu mlandu utsimikizike.


Wotembereredwa iye wakukantha mnansi wake m'tseri. Ndi anthu onse anene, Amen.


Pa mkulu usalandire chomnenera, koma pakhale mboni ziwiri kapena zitatu.


Munthu wopeputsa chilamulo cha Mose angofa opanda chifundo pa mboni ziwiri kapena zitatu:


Ndipo ndidzalamulira mboni zanga ziwiri, ndipo zidzanenera masiku chikwi chimodzi ndi mazana awiri amphambu makumi asanu ndi limodzi, zovala chiguduli.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa