Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 33:55 - Buku Lopatulika

55 Koma mukapanda kupirikitsa okhala m'dziko pamaso panu, pamenepo iwo amene muwalola atsale adzakhala ngati zotwikira m'maso mwanu, ndi minga m'mbali zanu, nadzakuvutani m'dziko limene mukhalamo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

55 Koma mukapanda kupirikitsa okhala m'dziko pamaso panu, pamenepo iwo amene muwalola atsale adzakhala ngati zotwikira m'maso mwanu, ndi minga m'mbali zanu, nadzakuvutani m'dziko limene mukhalamo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

55 Koma mukapanda kupirikitsa nzika zam'dzikomo pamene mukufika, amene mwaŵalola kuti atsalirewo adzakhala ngati zisonga zokubayani m'maso, ndiponso ngati minga m'mbali mwanu, ndipo adzakuvutani m'dziko m'mene mukakhalemo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

55 “ ‘Koma ngati simukathamangitsa nzika zimene zili mʼdzikomo, amene mukawalole kukhalamo adzakhala ngati zisonga mʼmaso mwanu ndi ngati minga mʼmbali mwanu. Adzakubweretserani mavuto mʼdziko limene mudzakhalemolo.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 33:55
11 Mawu Ofanana  

Asakhale m'dziko lako iwowa, kuti angakulakwitse pa Ine; pakuti ukatumikira milungu yao, kudzakukhalira msampha ndithu.


Ndipo nyumba ya Israele siidzakhalanso nayo mitungwi yolasa, kapena minga yaululu ya aliyense wakuizinga ndi kuipeputsa; motero adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.


Ndipo kudzakhala kuti monga ndinayesa kuchitira iwowa, ndidzakuchitirani inu.


Ndipo kuti ndingakwezeke koposa, chifukwa cha ukulu woposa wa mavumbulutso, kunapatsidwa kwa ine munga m'thupi, ndiye mngelo wa Satana kuti anditundudze, kuti ndingakwezeke koposa.


Ndipo mudzatha mitundu yonse ya anthu amene Yehova Mulungu wanu adzapereka kwa inu; diso lanu lisawachitire chifundo; musamatumikira milungu yao; pakuti uku kudzakuchitirani msampha.


Popeza adzapatutsa mwana wanu aleke kunditsata Ine, kuti atumikire milungu ina; potero Yehova adzapsa mtima pa inu, ndipo adzakuonongani msanga.


osalowa pakati pa amitundu awa otsala mwa inu; kapena kutchula dzina la milungu yao; osalumbiritsa nalo, kapena kuitumikira, kapena kuigwadira;


Chifukwa chakenso ndinati, Sindidzawapirikitsa kuwachotsa pamaso panu; koma adzakhala ngati minga m'nthiti zanu, ndi milungu yao idzakhalira inu msampha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa