Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 31:28 - Buku Lopatulika

28 Ndipo usonkhetse anthu ankhondo akutuluka kunkhondo apereke kwa Yehova: munthu mmodzi mwa anthu mazana asanu, mwa ng'ombe, mwa abulu, mwa nkhosa ndi mbuzi, momwemo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

28 Ndipo usonkhetse anthu ankhondo akutuluka kunkhondo apereke kwa Yehova: munthu mmodzi mwa anthu mazana asanu, mwa ng'ombe, mwa abulu, mwa nkhosa ndi mbuzi, momwemo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

28 Pa gawo la ankhondowo, mutengeko gawo la Chauta, pa zofunkha mazana asanu aliwonse mutengeko chimodzi, pa akapolo, pa ng'ombe, pa abulu ndi pa nkhosa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

28 Pa gawo la ankhondowo, mutengeko gawo la Yehova, pa zofunkha 500 zilizonse mutengeko chimodzi, pa akapolo, ngʼombe, bulu ndi nkhosa.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 31:28
18 Mawu Ofanana  

ayamikike Mulungu Wamkulukulu amene wapereka adani ako m'dzanja lako. Ndipo anampatsa iye limodzi la magawo khumi la zonse.


Izi zomwe mfumu Davide anazipatulira Yehova, pamodzi ndi siliva ndi golide adazitenga kwa amitundu onse, kwa Edomu, ndi kwa Mowabu, ndi kwa ana a Amoni, ndi kwa Afilisti, ndi kwa Amaleke.


Naphera Yehova nsembe tsiku lija za zofunkha adabwera nazo, ng'ombe mazana asanu ndi awiri, ndi nkhosa zikwi zisanu ndi ziwiri.


Nthawi imeneyo mphatso idzaperekedwa kwa Yehova wa makamu, mtundu wa anthu aatali ndi osalala, yochokera kwa mtundu woopsa chikhalire chao; mtundu umene uyesa dziko ndi kupondereza pansi, umene dziko lake nyanja ziligawa, kumalo a dzina la Yehova wa makamu, phiri la Ziyoni.


Malonda ake ndi mphotho yake zidzakhala zopatulikira Yehova; sizidzasungidwa kapena kuikidwa; chifukwa malonda ake adzakhala kwa iwo, amene akhala pamaso pa Yehova, kuti adye mokwana, navale chaulemu.


Zoonadi, zisumbu zidzandilindira Ine; zidzayamba ndi ngalawa za Tarisisi kutenga ana ako aamuna kutali, golide wao ndi siliva wao pamodzi nao, chifukwa cha dzina la Yehova Mulungu wako, ndi chifukwa cha Woyera wa Israele, popeza Iye wakukometsa iwe.


Ndipo taonani, ndawaninkha ana a Levi limodzi la magawo khumi mwa zonse mu Israele, likhale cholowa chao, mphotho ya pa ntchito yao alikuichita, ntchito ya chihema chokomanako.


Unenenso ndi Alevi, nuti nao, Pamene mulandira kwa ana a Israele, limodzi la magawo khumi limene ndakupatsani likhale cholowa chanu chochokera kwao, muziperekako nsembe yokweza ya Yehova, limodzi la magawo khumi la limodzi la magawo khumi.


Uzitenge ku gawo lao, ndi kuzipereka kwa Eleazara wansembe, zikhale nsembe yokweza ya Yehova.


Ndipo ku gawo la ana a Israele utenge munthu mmodzi mwa anthu makumi asanu, mwa ng'ombe, mwa abulu, mwa nkhosa ndi mbuzi, mwa zoweta zonse, momwemo; nuzipereke kwa Alevi, akusunga udikiro wa chihema cha Yehova.


mwa gawolo la ana a Israele Mose anatenga munthu mmodzi mwa makumi asanu, ndi zoweta momwemo, nazipereka kwa Alevi, akusunga udikiro wa chihema cha Yehova; monga Yehova adamuuza Mose.


Nanena iwo, Cha Kaisara. Pomwepo Iye anati kwa iwo, Chifukwa chake patsani kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.


Koma siliva yense, ndi golide yense, ndi zotengera za mkuwa ndi chitsulo zikhala chopatulikira Yehova; zilowe m'mosungira chuma cha Yehova.


Ndipo anatentha mzinda ndi moto, ndi zonse zinali m'mwemo; koma siliva ndi golide ndi zotengera zamkuwa ndi zachitsulo anaziika m'mosungira chuma cha nyumba ya Yehova.


Ndipo tsiku lija Yoswa anawasandutsa akutema nkhuni, ndi otungira madzi msonkhanowo, ndi guwa la nsembe la Yehova, mpaka lero lino, pamalopo akadzasankha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa