Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 29:39 - Buku Lopatulika

39 Izi muzikonzera Yehova mu zikondwerero zanu zoikika, pamodzi ndi zowinda zanu, ndi zopereka zanu zaufulu, za nsembe zanu zopsereza, ndi za nsembe zanu zaufa, ndi za nsembe zanu zothira, ndi za nsembe zanu zoyamika.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

39 Izi muzikonzera Yehova mu zikondwerero zanu zoikika, pamodzi ndi zowinda zanu, ndi zopereka zanu zaufulu, za nsembe zanu zopsereza, ndi za nsembe zanu zaufa, ndi za nsembe zanu zothira, ndi za nsembe zanu zoyamika.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

39 “Zimenezi ndizo zimene mudzapereke kwa Chauta pa masiku osankhidwa achikondwerero, kuwonjezera pa zopereka zanu zimene mudazilumbirira ndi pa zopereka zanu zaufulu: nsembe zanu zopsereza, nsembe zanu zaufa, nsembe zanu zachakumwa ndi nsembe zanu zachiyanjano.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

39 “ ‘Kuwonjezera pa zopereka zimene munalumbirira ndi pa zopereka zanu zaufulu, muzipereka zimenezi kwa Yehova pa masiku osankhika a chikondwerero chanu. Nsembe zanu zachakumwa ndi nsembe zanu zachiyanjano.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Numeri 29:39
20 Mawu Ofanana  

ndi kupereka nsembe zopsereza zonse kwa Yehova, za masabata, za pokhala mwezi, za nyengo zoikika, kuwerenga kwake monga mwa lemba lake, kosalekeza pamaso pa Yehova;


Ndipo Kore mwana wa Imina Mlevi, wa kuchipata cha kum'mawa, anayang'anira zopereka zaufulu za Mulungu, kugawira nsembe zokweza za Yehova, ndi zopatulika kwambiri.


Naikanso gawo la mfumu lotapa pa chuma chake la nsembe zopsereza, ndilo la nsembe zopsereza za m'mawa ndi madzulo, ndi la nsembe zopsereza za masabata, ndi za pokhala mwezi, ndi za nyengo zoikika, monga mulembedwa m'chilamulo cha Yehova.


Nachita chikondwerero cha Misasa monga kwalembedwa, napereka nsembe yopsereza tsiku ndi tsiku mawerengedwe ake, monga mwa lamulo lake la tsiku lake pa tsiku lake;


atatero anaperekanso nsembe yopsereza yosalekeza, ndi za pokhala mwezi, ndi za nyengo zoikika zonse za Yehova zopatulika, ndi za munthu yense wopereka nsembe yaufulu kwa Yehova mwaufulu.


kulipereka mkate woonekera, ndi nsembe yaufa yosaleka, ndi nsembe yopsereza yosaleka, ya masabata, ya pokhala miyezi, kuliperekera nyengo zoikika ndi zopatulikira, ndi nsembe za zolakwa za kutetezera Israele zoipa, ndi ntchito zonse za nyumba ya Mulungu wathu.


Masiku anu okhala mwezi ndi nthawi ya zikondwerero zanu mtima wanga uzida; zindivuta Ine; ndalema ndi kupirira nazo.


Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Nyengo zoikika za Yehova zimene muzilalikira zikhale misonkhano yopatulika, ndizo nyengo zanga zoikika.


Musamagwira ntchito iliyonse tsiku limenelo; pakuti ndilo tsiku la chitetezero, kuchita chotetezera inu pamaso pa Yehova Mulungu wanu.


pamodzi ndi masabata a Yehova, ndi pamodzi ndi mphatso zanu, ndi pamodzi ndi zowinda zanu zonse, ndi pamodzi ndi zopereka zaufulu zanu, zimene muzipereka kwa Yehova.


Ndipo chilamulo cha nsembe zoyamika, zimene azibwera nazo kwa Yehova ndi ichi:


Inde, mungakhale mupereka kwa Ine nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zaufa, sindidzazilandira Ine; ndi nsembe zoyamika za ng'ombe zanu zonenepa, sindidzazisamalira Ine.


Uza ana a Israele, nuti nao, Muzisamalira kubwera nacho kwa Ine chopereka changa, chakudya changa cha nsembe zanga zamoto, cha fungo lokoma, pa nyengo yake yoikika.


ndi tonde mmodzi wa nsembe yauchimo; pamodzi ndi nsembe yopsereza yosakeleza, ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira.


Ndipo Mose ananena ndi ana a Israele monga mwa zonse Yehova adamuuza Mose.


Ichi ndi chilamulo cha Mnaziri wakuwinda, ndi cha chopereka chake cha Yehova chifukwa cha kusala kwake, pamodzi nacho chimene dzanja lake likachipeza; azichita monga mwa chowinda chake anachiwinda, mwa chilamulo cha kusala.


Chifukwa chake mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.


ndi kubwera nazo kumeneko nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zanu zophera, ndi magawo anu onse a magawo khumi, ndi nsembe yokweza ya dzanja lanu, ndi zowinda zanu, ndi nsembe zanu zaufulu, ndi zoyamba kubadwa za ng'ombe zanu, ndi za nkhosa ndi mbuzi zanu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa