Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Nehemiya 9:28 - Buku Lopatulika

28 Koma atapumula, anabwereza kuchita choipa pamaso panu; chifukwa chake munawasiya m'dzanja la adani ao amene anachita ufumu pa iwo; koma pobwera iwo ndi kufuula kwa Inu, munamva mu Mwamba ndi kuwapulumutsa kawirikawiri, monga mwa chifundo chanu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

28 Koma atapumula, anabwereza kuchita choipa pamaso panu; chifukwa chake munawasiya m'dzanja la adani ao amene anachita ufumu pa iwo; koma pobwera iwo ndi kufuula kwa Inu, munamva m'Mwamba ndi kuwapulumutsa kawirikawiri, monga mwa chifundo chanu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

28 Koma atakhala pa mtendere, adayambanso kuchimwa pamaso panu, ndipo mudaŵaperekanso kwa adani ao, kotero kuti adani aowo ankaŵalamulira. Komabe pamene ankabwerera ndi kumalira Inu, Inuyo munkaŵamvera muli Kumwambako. Motero nthaŵi zambiri munkaŵapulumutsa chifukwa cha chifundo chanu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

28 “Koma akangokhala pa mtendere ankayambanso kuchita zoyipa pamaso panu. Choncho munkawapereka mʼmanja mwa adani awo amene ankawalamulira. Komabe pamene ankabwerera ndi kumalira kwa Inu, Inu munkawamva muli kumwambako. Chifukwa cha chifundo chanu chochuluka, nthawi zonse munkawapulumutsa.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 9:28
12 Mawu Ofanana  

pamenepo mverani Inu mu Mwamba mokhala Inu, ndi kukhululukira, ndi kuchita, ndi kubwezera munthu yense monga njira zake zonse, amene Inu mumdziwa mtima wake, popeza Inu, Inu nokha, mudziwa mitima ya ana onse a anthu;


Adani ao anawasautsanso, nawagonjetsa agwire mwendo wao.


Natikwatula kwa otisautsa; pakuti chifundo chake nchosatha.


Tayang'anani kunsi kuchokera kumwamba, taonani pokhala panu poyera, ndi pa ulemerero wanu, changu chanu ndi ntchito zanu zamphamvu zili kuti? Mwanditsekerezera zofunafuna za mtima wanu ndi chisoni chanu.


Koma kunali atafa woweruzayo anabwerera m'mbuyo, naposa makolo ao ndi kuchita moipitsa, ndi kutsata milungu ina kuitumikira ndi kuigwadira, sanaleke kanthu ka machitidwe ao kapena ka njira yao yatcheni.


Motero anagonjetsa Mowabu tsiku lija pansi padzanja la Israele. Ndipo dziko linapumula zaka makumi asanu ndi atatu.


Ndipo ana a Israele anaonjeza kuchita choipa pamaso pa Yehova, atafa Ehudi.


Adani anu onse, Yehova, atayike momwemo. Koma iwo akukonda Inu akhale ngati dzuwa lotuluka mu mphamvu yake. Ndipo dziko linapumula zaka makumi anai.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa