osawerenga akapolo ao aamuna ndi aakazi, ndiwo zikwi zisanu ndi ziwiri mphambu mazana atatu ndi makumi atatu kudza asanu ndi awiri; ndipo anakhala nao aamuna ndi aakazi oimbira mazana awiri.
Ndipo amitundu onse adzamtumikira iye, ndi mwana wake, ndi mdzukulu wake, mpaka yafika nthawi ya dziko lake; ndipo amitundu ambiri ndi mafumu aakulu adzamuyesa iye mtumiki wao.