Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Nehemiya 13:31 - Buku Lopatulika

31 ndi chopereka cha nkhuni pa nthawi zoikika, ndi wa zipatso zoyamba. Mundikumbukire, Mulungu wanga, chindikomere.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

31 ndi chopereka cha nkhuni pa nthawi zoikika, ndi wa zipatso zoyamba. Mundikumbukire, Mulungu wanga, chindikomere.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

31 Chinanso, ndidalamula kuti nkhuni ndi zipatso zoyamba kucha azipereke pa nthaŵi yoyenera. Inu Mulungu wanga, mukumbukire zonsezi ndipo mundikomere mtima.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

31 Ndiponso kupereka nkhuni ndi zipatso zoyamba kucha pa nthawi yake. Ndikumbukireni pondikomera mtima, Inu Mulungu wanga.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 13:31
10 Mawu Ofanana  

Ndipo tinalota maere, ansembe, Alevi, ndi anthu, a chopereka cha nkhuni, kubwera nazo kunyumba ya Mulungu wathu, monga mwa nyumba za makolo athu, pa nyengo zoikika chaka ndi chaka, kuzisonkha paguwa la nsembe la Yehova Mulungu wathu, monga mulembedwa m'chilamulo;


ndi kubwera nazo zipatso zoyamba za nthaka, ndi zoyamba za zipatso zonse za mtengo uliwonse chaka ndi chaka, ku nyumba ya Yehova;


Ndipo wansembe mwana wa Aroni azikhala ndi Alevi, polandira Alevi limodzilimodzi la magawo khumi; ndi Alevi azikwera nalo limodzi la magawo khumi mwa limodzilimodzi la magawo khumi kunyumba ya Mulungu wathu, kuzipinda, kunyumba ya chuma.


Mundikumbukire Mulungu wanga mwa ichi, nimusafafanize zokoma zanga ndinazichitira nyumba ya Mulungu wanga, ndi maudikiro ake.


Ndipo ndinauza Alevi kuti adziyeretse, nabwere, nasunge pazipata kupatula tsiku la Sabata. Mundikumbukire ichinso, Mulungu wanga, ndi kundileka monga mwa chifundo chanu chachikulu.


Mundikumbukire Mulungu, zindikomere zonse ndinachitira anthu awa.


Mundikumbukire, Yehova, monga momwe muvomerezana ndi anthu anu; mundionetsa chipulumutso chanu:


Musakumbukire zolakwa za ubwana wanga kapena zopikisana nanu. Mundikumbukire monga mwa chifundo chanu, chifukwa cha ubwino wanu, Yehova.


Ndipo ananena, Yesu, ndikumbukireni m'mene mulowa Ufumu wanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa