Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Nehemiya 12:38 - Buku Lopatulika

38 Ndi gulu lina la oyamikira linamuka mokomana nao, ndi ine ndinawatsata, pamodzi ndi limodzi la magawo awiri la anthu palinga, napitirira pa Nsanja ya Ng'anjo, mpaka kulinga lachitando;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

38 Ndi gulu lina la oyamikira linamuka mokomana nao, ndi ine ndinawatsata, pamodzi ndi limodzi la magawo awiri la anthu palinga, napitirira pa Nsanja ya Ng'anjo, mpaka kulinga lachitando;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

38 Mdipiti wina wa anthu othokoza Mulungu udadzera chakumanzere kwa khomalo, ndipo ine ndidautsata pambuyo, poyenda pa khoma pamodzi ndi theka lina la akuluakulu. Tidapitirira Nsanja ya Ng'anjo, kukafika ku Khoma Lotambasuka.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

38 Gulu loyimba lachiwiri linadzera mbali ya kumanzere kwa khomalo. Tsono ine ndi theka lina la atsogoleri aja tinkalitsata pambuyo tikuyenda pamwamba pa khomalo. Tinapitirira Nsanja ya Ngʼanjo mpaka ku Khoma Lotambasuka.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 12:38
3 Mawu Ofanana  

Pamenepo ndinakwera nao akulu a Yuda pa lingali, ndinaikanso oyamikira magulu awiri akulu oyenda molongosoka; lina loyenda ku dzanja lamanja palinga kunka ku Chipata cha Kudzala;


Malikiya mwana wa Harimu, ndi Hasubu mwana wa Pahatimowabu, anakonza gawo lina, ndi Nsanja ya Ng'anjo.


Pambali pake anakonza Uziyele mwana wa Haraya, wa iwo osula golide. Ndi padzanja pake anakonza Hananiya, wa iwo osanganiza zonunkhira; nalimbikitsa Yerusalemu mpaka linga lachitando.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa