Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Nehemiya 12:37 - Buku Lopatulika

37 ndi ku Chipata cha ku Chitsime, ndi kundunji kwao, anakwerera pa makwerero a mzinda wa Davide, potundumuka linga, popitirira pa nyumba ya Davide, mpaka ku Chipata cha Madzi kum'mawa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

37 ndi ku Chipata cha ku Chitsime, ndi kundunji kwao, anakwerera pa makwerero a mudzi wa Davide, potundumuka linga, popitirira pa nyumba ya Davide, mpaka ku Chipata cha Madzi kum'mawa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

37 Kuchokera ku Chipata cha Kasupe, adakwera pa makwerero opita ku mzinda wa Davide, pa njira yotsatira khoma, chakumtunda kwa nyumba ya Davide, mpaka kukafika ku Chipata cha Madzi, kuvuma kwa mzinda wa Yerusalemu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

37 Kuchokera ku Chipata cha Kasupe anayenda nakakwera makwerero opita ku mzinda wa Davide pa njira yotsatira khoma, chakumtundu kwa nyumba ya Davide mpaka ku Chipata cha Madzi, mbali ya kummawa.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 12:37
7 Mawu Ofanana  

Ndipo ndinapitirira kunka ku Chipata cha Chitsime, ndi ku Dziwe la Mfumu; koma popita nyama ili pansi panga panaichepera.


Koma antchito a m'kachisi okhala mu Ofele anakonza kufikira kumalo a pandunji pa Chipata cha Madzi kum'mawa, ndi nsanja yosomphokayo.


Ndipo anthu onse anasonkhana ngati munthu mmodzi kukhwalala lili ku Chipata cha Madzi, namuuza Ezara mlembi atenge buku la chilamulo cha Mose, chimene Yehova adalamulira Israele.


Natuluka anthu, nakazitenga, nadzimangira misasa, yense pa tsindwi la nyumba yake, ndi m'mabwalo ao, ndi m'mabwalo a nyumba ya Mulungu, ndi pa khwalala la Chipata cha Madzi, ndi pa khwalala la Chipata cha Efuremu.


Nawerenga m'menemo pa khwalala lili ku Chipata cha Madzi kuyambira mbandakucha kufikira msana, pamaso pa amuna ndi akazi, ndi iwo okhoza kuzindikira; ndi anthu onse anatcherera khutu buku la chilamulo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa