Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 11:22 - Buku Lopatulika

22 Ndipo woyang'anira wa Alevi mu Yerusalemu ndiye Uzi mwana wa Bani, mwana wa Hasabiya, mwana wa Mataniya, mwana wa Mika; mwa ana a Asafu oimbira ena anayang'anira ntchito ya m'nyumba ya Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Ndipo woyang'anira wa Alevi m'Yerusalemu ndiye Uzi mwana wa Bani, mwana wa Hasabiya, mwana wa Mataniya, mwana wa Mika; mwa ana a Asafu oimbira ena anayang'anira ntchito ya m'nyumba ya Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Kapitao wa Alevi ku Yerusalemu anali Uzi, mwana wa Bani, mwana wa Hasabiya, mwana wa Mataniya, mwana wa Mika. Anali mmodzi mwa zidzukulu za a Asafu, amene anali oimba nyimbo zofunika pa miyambo ya m'Nyumba ya Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Wamkulu wa Alevi mu Yerusalemu anali Uzi mwana wa Bani, mwana wa Hasabiya, mwana wa Mataniya, mwana wa Mika. Uzi anali mmodzi wa zidzukulu za Asafu, amene anali oyimba nyimbo pa nthawi zachipembedzo mʼNyumba ya Mulungu.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 11:22
19 Mawu Ofanana  

Ndipo Mefiboseti anali ndi mwana wamwamuna wamng'ono, dzina lake ndiye Mika. Ndipo onse akukhala m'nyumba ya Ziba anali anyamata a Mefiboseti.


ndi Hasabiya, ndi pamodzi naye Yesaya wa ana a Merari, abale ake ndi ana ao makumi awiri;


Mika, Rehobu, Hasabiya,


Hodiya, Bani, Beninu.


Seraya mwana wa Hilikiya, mwana wa Mesulamu, mwana wa Zadoki, mwana wa Meraiyoti, mwana wa Ahitubi mtsogoleri wa m'nyumba ya Mulungu;


ndi abale ao, ngwazi zamphamvu, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu; ndi woyang'anira wao ndiye Zabidiele mwana wa Hagedolimu.


Ndi Yowele mwana wa Zikiri ndiye woyang'anira wao, ndi Yuda mwana wa Hasenuwa ndiye wothandizana naye, poyang'anira mzinda.


ndi ana ena a ansembe ndi malipenga: Zekariya mwana wa Yonatani, mwana wa Semaya, mwana wa Mataniya, mwana wa Mikaya, mwana wa Zakuri, mwana wa Asafu,


ndi Maaseiya, ndi Semaya, ndi Eleazara, ndi Uzi, ndi Yehohanani, ndi Malikiya, ndi Elamu, ndi Ezere. Ndipo oimbira anaimbitsa Yezeraya ndiye woyang'anira wao.


Pakuti m'masiku a Davide ndi Asafu kalelo kunali mkulu wa oimbira, ndi wa nyimbo zolemekeza ndi zoyamikira Mulungu.


Ndinaikanso osunga chuma, asunge nyumba za chuma: Selemiya wansembe, ndi Zadoki mlembi; ndi wa Alevi, Pedaya; ndi wakuwathandiza, Hanani mwana wa Zakuri, mwana wa Mataniya; popeza anayesedwa okhulupirika ndi udindo wao, ndiwo kugawira abale ao.


Potsatizana naye anakonza Alevi, Rehumu mwana wa Bani. Pambali pake anakonza Hasabiya mkulu wa dera lina la dziko la Keila, kukonzera dziko lake.


Ndi Yesuwa, ndi Bani, ndi Serebiya, Yamini, Akubu, Sabetai, Hodiya, Maaseiya, Kelita, Azariya, Yozabadi, Hanani, Pelaya, ndi Alevi, anadziwitsa anthu chilamulocho; ndi anthu anali chilili pamalo pao.


Tadzichenjerani nokha, ndi gulu lonse, pamenepo Mzimu Woyera anakuikani oyang'anira, kuti muwete Mpingo wa Mulungu, umene anaugula ndi mwazi wa Iye yekha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa