Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Nehemiya 10:28 - Buku Lopatulika

28 Ndi anthu otsala, ansembe, Alevi, odikira, oimbira, antchito a m'kachisi, ndi onse anadzisiyanitsawo pa mitundu ya anthu a m'dziko kutsata chilamulo cha Mulungu, akazi ao, ana ao aamuna ndi aakazi, yense wodziwa ndi wozindikira,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

28 Ndi anthu otsala, ansembe, Alevi, odikira, oimbira, Anetini, ndi onse anadzisiyanitsawo pa mitundu ya anthu a m'dziko kutsata chilamulo cha Mulungu, akazi ao, ana ao aamuna ndi aakazi, yense wodziwa ndi wozindikira,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

28 Ife otsalafe, ansembe, Alevi, alonda a pa Nyumba ya Mulungu, oimba nyimbo, atumiki a ku Nyumba ya Mulungu, ndi onse amene ankadzipatula kwa mitundu ina ya anthu ya m'maiko achilendo, kuti atsate Malamulo a Mulungu, tonse, pamodzi ndi akazi athu, ana athu ndi onse amene ali ndi nzeru zokwanira,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

28 Ife otsalafe, ndiye kuti ansembe, Alevi, alonda a ku Nyumba ya Mulungu, oyimba nyimbo, ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu, onse amene anadzipatula pakati pa anthu a mitundu ina kuti atsate malamulo a Yehova, pamodzi ndi akazi athu, ana athu ndi onse amene ali ndi nzeru,

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 10:28
16 Mawu Ofanana  

Ndipo ansembe, ndi Alevi, ndi anthu ena, ndi oimbira, ndi odikira, ndi antchito a m'kachisi, anakhala m'midzi mwao, ndi Aisraele onse m'midzi mwao.


Ndipo ana a Israele obwera kundende, ndi yense wakudzipatulira kuchokera chonyansa cha amitundu, kutsata iwowa, kufuna Yehova Mulungu wa Israele, anadza,


Maluki, Harimu, Baana.


Ndipo kunali, atamva chilamulocho, anasiyanitsa pa Israele anthu osokonezeka onse.


Ndipo Ezara wansembe anabwera nacho chilamulo pamaso pa msonkhano, ndiwo amuna ndi akazi, ndi yense wakumva ndi kuzindikira tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiwiri.


Nadzipatula a mbumba ya Israele kwa alendo onse, naimirira, nawulula zochimwa zao, ndi mphulupulu za makolo ao.


Pakuti Mulungu ndiye mfumu ya dziko lonse lapansi; imbirani ndi chilangizo.


Usalankhule mwanthuku mtima wako, usafulumire kunena kanthu pamaso pa Mulungu; pakuti Mulungu ali kumwamba, iwe uli pansi; chifukwa chake mau ako akhale owerengeka.


Ndipo udzalumbira, Pali Yehova m'zoonadi, m'chiweruziro, ndi m'chilungamo; ndipo mitundu ya anthu idzadzidalitsa mwa Iye, ndipo mwa Iye adzatamandira.


Koma ndanena nanu, Mudzalandira dziko lao inu, ndipo Ine ndilipereka kwa inu likhale lanu, ndilo dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; Ine ndine Yehova Mulungu wanu amene ndinakusiyanitsani ndi mitundu ina ya anthu.


Paulo, kapolo wa Yesu Khristu, mtumwi woitanidwa, wopatulidwa kukanena Uthenga Wabwino wa Mulungu,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa