Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Nahumu 3:3 - Buku Lopatulika

3 munthu wokwera pa kavalo, ndi lupanga lonyezimira, ndi mkondo wong'anipa; ndi aunyinji ophedwa, ndi chimulu cha mitembo, palibe kutha zitanda; angokhumudwa ndi zitanda;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 munthu wokwera pa kavalo, ndi lupanga lonyezimira, ndi mkondo wong'anipa; ndi aunyinji ophedwa, ndi chimulu cha mitembo, palibe kutha zitanda; angokhumudwa ndi zitanda;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Okwera pa akavalo akuthamanga, malupanga ali ŵaliŵali, mikondo ili phuliphuli. Afa anthu ambiri, mitembo yati vuu, yosaŵerengeka, anthu kumaphunthwa pa mitemboyo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Kuthamanga kwa anthu okwera pa akavalo, kungʼanima kwa malupanga ndi kunyezimira kwa mikondo! Anthu ambiri ophedwa, milumilu ya anthu akufa, mitembo yosawerengeka, anthu akupunthwa pa mitemboyo.

Onani mutuwo Koperani




Nahumu 3:3
10 Mawu Ofanana  

Ndipo anamuingitsa munthuyo; nakhazika akerubi cha kum'mawa kwake kwa munda wa Edeni, ndi lupanga lamoto lakuzungulira ponsepo, lakusunga njira ya ku mtengo wa moyo.


Ndipo kunali, usiku womwewo mthenga wa Yehova anatuluka, nakantha m'misasa ya Aasiriya zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu kudza zisanu, ndipo pouka anthu mamawa, taonani, onsewo ndi mitembo.


Ophedwa aonso adzatayidwa kunja, ndipo kununkha kwa mitembo yao kudzamveka, ndipo mapiri adzasungunuka ndi mwazi wao.


Ndipo mthenga wa Yehova anatuluka, naphaipha m'zithando za Asiriya, zikwi zana ndi makumi asanu ndi atatu ndi zisanu, ndipo pamene anthu anauka mamawa, taonani, onse ndiwo mitembo.


Pakuti Yehova adzatsutsana ndi moto, ndi lupanga lake, ndi anthu onse; ndi ophedwa a Yehova adzakhala ambiri.


Udzagwa pa mapiri a Israele, iwe ndi magulu ako onse, ndi mitundu ya anthu okhala ndi iwe; ndidzakupereka kwa mbalame zolusa za mitundu yonse, ndi kwa zilombo zakuthengo, akuyese chakudya.


Ndipo adzakhumudwitsana monga pothawa lupanga, wopanda wakuwalondola; ndipo mudzakhala opanda mphamvu yakuima pamaso pa adani anu.


Magaleta achita mkokomo m'miseu, akankhana m'makwalala; maonekedwe ao akunga miuni, athamanga ngati mphezi.


Dzuwa ndi mwezi zinaima njera mokhala mwao; pa kuunika kwa mivi yanu popita iyo. Pa kung'anipa kwa nthungo yanu yonyezimira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa