Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Nahumu 3:1 - Buku Lopatulika

1 Tsoka mzinda wa mwazi! Udzala nao mabodza ndi zachifwamba; zachifwamba sizidukiza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Tsoka mudzi wa mwazi! Udzala nao mabodza ndi zachifwamba; zachifwamba sizidukiza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Tsoka kwa mzinda wokhetsa magazi a anthu ambiri, mzinda wodzaza ndi mabodza ndi zakuba, wokonda kufunkha mosalekeza.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Tsoka kwa mzinda wopha anthu, mzinda wodzaza ndi mabodza, mzinda wodzaza ndi anthu olanda zinthu anzawo, mu mzinda mʼmene simusowa anthu osautsidwa nthawi zonse!

Onani mutuwo Koperani




Nahumu 3:1
11 Mawu Ofanana  

Musakhulupirire kusautsa, ndipo musatama chifwamba; chikachuluka chuma musakhazikepo mitima yanu.


Pa nthawi ya madzulo, taonani kuopsa; kusanache, iwo palibe. Ili ndi gawo la iwo amene atifunkha ndi ichi chiwagwera omwe alanda zathu.


Iwo sadzamwa vinyo ndi kuimba nyimbo; chakumwa chaukali chidzawawa kwa iwo amene achimwa.


Ndani anapereka Yakobo, kuti afunkhidwe, ndi Israele, kuti awawanyidwe? Kodi si Yehova? Iye amene tamchimwira, ndi amene iwo anakonda kuyenda m'njira zake, ngakhale kumvera chiphunzitso chake.


Koma kulumbira, ndi kunama, ndi kupha, ndi kuba, ndi kuchita chigololo; aboola, ndi mwazi ukhudzana nao mwazi.


Mkangowo unamwetula zofikira ana ake, nusamira yaikazi yake, nudzaza mapanga ake ndi nyama, ngaka zake ndi zojiwa.


Taona, nditsutsana nawe, ati Yehova wa makamu, ndipo ndidzatentha magaleta ake mu utsi; ndi lupanga lidzadya misona yako ya mkango; ndipo ndidzachotsa zofunkha zako padziko lapansi, ndi mau a mithenga yako sadzamvekanso.


Tsoka iye wakumanga mzinda ndi mwazi, nakhazikitsa mzinda ndi chisalungamo!


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa