Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Nahumu 2:7 - Buku Lopatulika

7 Chatsimikizika, avulidwa, atengedwa, adzakazi ake alira ngati mau a nkhunda, nadziguguda pachifuwa pao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Chatsimikizika, avulidwa, atengedwa, adzakazi ake alira ngati mau a nkhunda, nadziguguda pachifuwa pao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Mfumukazi yake yatengedwa ukapolo. Adzakazi ake akulira ngati nkhunda, ndipo akudzigunda pa chifuwa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Zatsimikizika kuti mzinda utengedwa ndi kupita ku ukapolo. Akapolo aakazi akulira ngati nkhunda ndipo akudziguguda pachifuwa.

Onani mutuwo Koperani




Nahumu 2:7
9 Mawu Ofanana  

Iwo adzadzimenya pazifuwa chifukwa cha minda yabwino, chifukwa cha mpesa wobalitsa.


Ndinalankhulalankhula ngati namzeze, pena chumba; Ndinalira maliro ngati nkhunda; maso anga analephera pogadamira kumwamba. Ambuye ndasautsidwa, mundiperekere chikoli.


Tonse tibangula ngati zilombo, ndi kulira maliro zolimba ngati nkhunda; tiyang'anira chiweruziro koma palibe; tiyang'anira chipulumutso koma chili patali ndi ife.


Ndipo akupulumuka mwa iwo adzapulumuka, koma adzakhala kumapiri ngati njiwa za kuzigwa, onse akubuula, aliyense m'mphulupulu zake.


Pa zipata za mitsinje patseguka, ndi chinyumba chasungunuka.


Taona, anthu ako m'kati mwako akunga akazi, zipata za dziko lako zatsegulidwira adani ako papakulu; moto watha mipingiridzo yako.


Ndipo pamene Petro anali pansi m'bwalo, anadzapo mmodzi wa adzakazi a mkulu wa ansembe;


Ndipo unamtsata unyinji waukulu wa anthu, ndi wa akazi amene anadziguguda pachifuwa, namlirira Iye.


Ndipo makamu onse osonkhana kudzapenya ichi, pamene anaona zinachitikazo, anapita kwao ndi kudziguguda pachifuwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa