Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Nahumu 2:5 - Buku Lopatulika

5 Akumbukira omveka ake; akhumudwa m'kupita kwao, afulumira kulinga lake, ndi chotchinjiriza chakonzeka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Akumbukira omveka ake; akhumudwa m'kupita kwao, afulumira kulinga lake, ndi chotchinjiriza chakonzeka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Atsogoleri a ankhondo akuitanidwa, akubwera naphunthwa. Akuthamangira ku linga la mzinda, akuimika chipupa chodzitetezera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Iye akuyitanitsa asilikali ake wolemekezeka, koma iwo akubwera napunthwa. Akuthamangira ku linga la mzinda; akuyimika chodzitchinjirizira pamalo pake.

Onani mutuwo Koperani




Nahumu 2:5
9 Mawu Ofanana  

Iwo akonza pa gome lodyera, aika alonda, adya, namwa; ukani, akalonga inu, dzozani mafuta chikopa.


palibe amene adzalema, kapena adzaphunthwa mwa iwo, palibe amene adzaodzera kapena kugona tulo; ngakhale lamba la m'chuuno mwao silidzamasuka, kapena chomangira cha nsapato zao sichidzaduka;


Amitundu amva manyazi anu, dziko lapansi ladzala ndi kufuula kwanu; pakuti amphamvu akhumudwitsana, agwa onse awiri pamodzi.


Memezani amauta amenyane ndi Babiloni, onse amene akoka uta; mummangire iye zithando pomzungulira iye, asapulumuke mmodzi wake yense; mumbwezere iye monga mwa ntchito yake; monga mwa zonse wazichita, mumchitire iye; pakuti anamnyadira Yehova, Woyera wa Israele.


Pa zipata za mitsinje patseguka, ndi chinyumba chasungunuka.


Abusa ako aodzera, mfumu ya ku Asiriya; omveka ako apumula; anthu ako amwazika pamapiri, ndipo palibe wakuwasonkhanitsa.


munthu wokwera pa kavalo, ndi lupanga lonyezimira, ndi mkondo wong'anipa; ndi aunyinji ophedwa, ndi chimulu cha mitembo, palibe kutha zitanda; angokhumudwa ndi zitanda;


Akavalo ao aposa anyalugwe liwiro lao, aposa mimbulu ya madzulo ukali wao, ndipo apakavalo ao atanda; inde apakavalo ao afumira kutali; auluka ngati chiombankhanga chofulumira kudya.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa